Download as docx, pdf, or txt
Download as docx, pdf, or txt
You are on page 1of 12

Aefeso 1

1  2Ako. 1.1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa

oyera mtima amene ali m'Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu: 2
Chisomo kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi
Ambuye Yesu Khristu.

Madalitso a Mulungu mwa Yesu Khristu, Mpulumutsi wathu ndi mutu wa


Mpingo
3  1Pet. 1.3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu

Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa
Khristu; 4 Aro. 8.28; Akol. 1.22; 1Pet. 1.2, 20 monga anatisankha ife mwa Iye,

lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso
pake m'chikondi. 5 Aro. 8.29-30; Agal. 4.5 Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana
a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake, 6 Aro.
3.24 kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife
kwaufulu mwa Wokondedwayo. 7 Aro. 2.4; Akol. 1.14 Tili ndi maomboledwe

mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa
chisomo chake, 8chimene anatichulukitsira ife m'nzeru zonse, ndi
chisamaliro. 9 Akol. 1.26 Anatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake,
monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye, 10 Agal. 4.4;
Aef. 2.15; Afi. 2.9-10 kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo,

akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Khristu, za kumwamba, ndi za


padziko. 11 Mac. 20.32; Aef. 1.5 Mwa Iye tinayesedwa cholowa chake, popeza

tinakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse monga
mwa uphungu wa chifuniro chake; 12 Aef. 1.6, 14 kuti ife amene tinakhulupirira
Khristu kale tikayamikitse ulemerero wake. 13 Yoh. 1.17; Aef. 4.30 Mwa Iyeyo

inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi


kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa
lonjezano, 14 Mac. 20.28; 2Ako. 5.5 ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti

akeake akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike.


15Mwa ichi inenso, m'mene ndamva za chikhulupiriro cha mwa Ambuye Yesu
chili mwa inu ndi chikondi chanu, chimenenso mufikitsira oyera mtima
onse, 16 Afi. 1.3-4 sindileka kuyamika chifukwa cha inu, ndi kukumbukira inu
m'mapemphero anga; 17 Akol. 1.9 kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu,

Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti


mukamzindikire Iye; 18 Aef. 1.11; 2.12 ndiko kunena kuti maso a mitima yanu

awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuitana kwake nchiyani;


chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima, 19 Aef.
3.7 ndi chiyani ukulu woposa wa mphamvu yake ya kwa ife okhulupirira, monga
mwa machitidwe a mphamvu yake yolimba, 20 Mac. 2.24; 7.55-56 imene

anachititsa mwa Khristu, m'mene anamuukitsa kwa akufa, namkhazikitsa pa dzanja


lake lamanja m'zakumwamba, 21 Afi. 2.9-10 pamwamba pa ukulu wonse, ndi

ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lililonse lotchedwa, si m'nyengo
yino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza; 22 Mas. 8.6; Akol.
1.18 ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamtu
pa zonse, kwa Mpingo 23 Akol. 1.18; 2.14, 20 amene ali thupi lake, mdzazidwe

wa Iye amene adzaza zonse m'zonse.

Aefeso 2

Chipulumutso chichokera kuchisomo


1  Aef. 2.5 Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa,
ndi zochimwa zanu, 2 Akol. 1.21 zimene munayendamo kale, monga mwa

mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa


mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera; 3 Agal.
5.16 amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu,

ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo
chibadwire, monganso otsalawo; 4 Aef. 2.7; Aro. 2.4 koma Mulungu, wolemera

chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda


nacho, 5 Aro. 5.6, 8, 10 tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo
pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo), 6 Aef. 1.20 ndipo

anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba


mwa Khristu Yesu; 7 Tit. 3.4 kuti akaonetsere m'nthawi zilinkudza chuma

choposa cha chisomo chake, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Khristu
Yesu. 8 Yoh. 6.65; Aro. 3.24; 4.16 Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo

chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya
Mulungu; 9 Aro. 3.20, 28 chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu
aliyense. 10 1Ako. 3.9; 2Ako. 5.5, 17 Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa

mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti
tikayende m'menemo.
Ayuda ndi amitundu ayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa mtanda wa Khristu
11  Akol. 1.21 Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi,

otchedwa kusadulidwa ndi iwo otchedwa mdulidwe m'thupi, umene udachitika ndi


manja; 12 Yoh. 10.16; Agal. 4.8; Akol. 1.21 kuti nthawi ija munali opanda

Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi
mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko
lapansi. 13 Yes. 57.19; Mac. 2.39 Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene
munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu. 14 Mik.
5.5 Pakuti Iye ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti onse awiri akhale
mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati, 15 Akol. 2.14, 20 atachotsa udani

m'thupi lake, ndiwo mau a chilamulo cha kutchulako malangizo; kuti alenge
awiriwa mwa Iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kuchitapo
mtendere; 16 Akol. 1.20-22 ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi
limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo; 17 Yes. 57.19; Mac. 2.39 ndipo

m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi
mtendere kwa iwo apafupi; 18 Yoh. 14.6 kuti mwa Iye ife tonse awiri tili nao
malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi. 19 Afi. 3.20 Pamenepo ndipo

simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima
ndi a banja la Mulungu; 20 Mat. 16.18; 21.42 omangika pa maziko a atumwindi
aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya; 21 1Ako. 3.17; Aef. 4.15-
16 mwa Iye chimango chonse cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale
Kachisi wopatulika mwa Ambuye; 22 1Pet. 2.5 chimene inunso mumangidwamo

pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu.

Aefeso 3
Chinsinsi cha maitanidwe a amitundu
1  Mac. 21.33 Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende
wa KhristuYesu chifukwa cha inu amitundu, 2 Mac. 9.15 ngatitu munamva za
udindo wa chisomo cha Mulungu chimene anandipatsa ine cha kwa inu; 3 Agal.
1.12; Akol. 1.26-27 ndi umo anandizindikiritsa chinsinsicho mwa vumbulutso,

monga ndinalemba kale mwachidule, 4chimene mukhoza kuzindikira nacho,


pakuchiwerenga, chidziwitso changa m'chinsinsi cha Khristu, 5 Aef. 3.9; Aro.
16.25 chimene sanachizindikiritsa ana a anthu m'mibadwo ina, monga

anachivumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ake oyera mwa


Mzimu, 6 Agal. 3.28-29 kuti amitundu ali olowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi

ziwalo zinzathu za thupilo, ndi olandira nafe pamodzi palonjezano mwa Khristu
Yesu, mwa Uthenga Wabwino, 7 Akol. 1.23, 25 umene anandikhalitsa mtumiki

wake monga mwa mphatso ya chisomo cha Mulungu, chimene anandipatsa ine,
monga mwa machitidwe a mphamvu yake. 8 1Ako. 15.9 Kwa ine wochepa ndi

wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa


amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu; 9 Aef. 3.3 ndi kuwalitsira onse

adziwe makonzedwe a chinsinsicho, chimene chinabisika kuyambira kalekale mwa


Mulungu wolenga zonse; 10 1Tim. 3.16 kuti mu Mpingoazindikiritse tsopano kwa

akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya


Mulungu, 11 Yoh. 6.33, 62 monga mwa chitsimikizo mtima cha nthawi za nthawi,

chimene anachita mwa Khristu Yesu Ambuye wathu: 12amene tili naye


chokhazikika mtima ndi chiyandiko cholimbika, mwa chikhulupiriro cha pa
Iye. 13 Aef. 3.1 Mwa ichi ndipempha kuti musade mtima m'zisautso zanga

chifukwa cha inu, ndiwo ulemerero wanu.


Paulo apempherera Aefeso
14Chifukwa cha ichi ndipinda maondo anga kwa Atate, 15 Afi. 2.9-11 amene

kuchokera kwa Iye fuko lonse la m'mwamba ndi la padziko alitcha


dzina, 16 Akol. 1.11 kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni
inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu, 17 Yoh. 14.23 kuti Khristu

akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi
otsendereka m'chikondi, 18 Aef. 1.18 mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera
mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, 19 Akol. 2.9-10 ndi kuzama

nchiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti


mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu.
20  Aro. 16.25 Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse

zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa


ife, 21 Aro. 11.36 kwa Iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu,

kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.

Aefeso 4

Umodzi wa iwo a chikhulupiriro


1  Aef. 3.1; Akol. 1.10 Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa
Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao, 2 Mac. 20.19;
Afi. 2.3 ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera
chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi; 3 Akol. 3.14 ndi

kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha


mtendere. 4 1Ako. 12.4, 11 Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso
anakuitanani m'chiyembekezo chimodzi cha maitanidwe anu; 5 1Ako.
1.13 Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi, 6 1Ako.
8.6 Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa
onse, ndi m'kati mwa zonse. 7 Aro. 12.3, 6 Ndipo kwa yense wa ife chapatsika

chisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Khristu.


8  Mas. 68.18 Chifukwa chake anena,

M'mene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende,


naninkha zaufulu kwa anthu.
9  Yoh. 6.33, 62 Koma ichi, chakuti, Anakwera, nchiyani nanga koma kuti
anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko? 10 Mac. 1.9, 11 Iye wotsikayo ndiye

yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu


zonse. 11 1Ako. 12.28 Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi
ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; 12 1Ako. 12.7, 27 kuti akonzere
oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu; 13 Akol. 1.28;
2.2-3 kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa

chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa


msinkhu wa chidzalo cha Khristu. 14 Aheb. 13.9 Kuti tisakhalenso makanda,

ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi


tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa; 15 Zek.
8.16; 2Ako. 4.2; Akol. 1.18 koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule
m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu; 16 Akol.
2.19 kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi,

pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa


muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.
Kusiyana kwa kuyera mtima kwa Chikhristu ndi mayendedwe oipa a akunja
17  Aef. 2.1-2 Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye,

kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'chitsiru cha mtima


wao, 18 Aef. 2.12 odetsedwa m'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa

Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa
mitima yao; 19 Aro. 1.24, 26 amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse,

anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu


umbombo. 20Koma inu simunaphunzira Khristu chotero, 21 Aef. 1.13 ngatitu

mudamva Iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye, monga choonadi chili


mwa Yesu; 22 Aro. 6.6 kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu
wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; 23 Akol. 3.10 koma kuti
mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, 24 Akol.
3.10 nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu,

m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.


25  Aro. 12.5; Aef. 4.15 Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense
ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake. 26 Mas. 37.8 Kwiyani, koma
musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire, 27 Yak. 4.7 ndiponso musampatse
malo mdierekezi. 28 1Ate. 4.11 Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse

ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza
wosowa. 29 Akol. 3.8, 16 Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu,

koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse
chisomo kwa iwo akumva. 30 Yes. 63.10; Aef. 1.13 Ndipo musamvetse chisoni

Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye,


kufikira tsiku la maomboledwe. 31 Akol. 3.8, 19 Chiwawo chonse, ndi kupsa

mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso
choipa chonse. 32 Mrk. 11.25; 1Pet. 3.8-9 Koma mukhalirane okoma wina ndi

mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa


Khristu anakhululukira inu.

Aefeso 5

1  Mat. 5.45, 48 Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana


okondedwa; 2 Yoh. 13.34; 2Ako. 2.15; Agal. 2.20 ndipo yendani m'chikondi

monganso Khristuanakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu,


chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino. 3Koma
dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe
mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; 4 Aef. 4.29 kapena chinyanso, ndi

kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka


chiyamiko. 5 Agal. 5.19-21 Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena

wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa m'ufumu


wa Khristu ndi Mulungu. 6 Mat. 24.4 Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda

pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a


kusamvera. 7Chifukwa chake musakhale olandirana nao; 8 Yoh. 8.12; 12.36,
46 pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani

monga ana a kuunika, 9pakuti chipatso cha kuunika tichipeza m'ubwino wonse, ndi
chilungamo, ndi choonadi, 10kuyesera chokondweretsa Ambuye
nchiyani; 11 1Ako. 5.9, 11; 10.20 ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima
zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse; 12 Aro. 1.24, 26 pakuti
zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. 13 Yoh. 3.20-
21 Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse
chakuonetsa chili kuunika. 14 Yes. 60.1; Aro. 6.4-5; 13.11-12 Mwa ichi anena,

Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.
15  Akol. 4.5 Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru,
koma monga anzeru; 16akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. 17 1Ate.
4.3 Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye
nchiyani. 18 Miy. 20.1; Luk. 21.34 Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli
chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, 19 Mac. 16.25 ndi kudzilankhulira nokha

ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba
m'malimba Ambuye mumtima mwanu; 20 Mas. 34.1; Akol. 3.17 ndi kuyamika

Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye


wathu Yesu Khristu; 21 Afi. 2.3 ndi kumverana wina ndi mnzake m'kuopa

Khristu.
22  Akol. 3.18 Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera
Ambuye. 23 1Ako. 11.3 Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso

Khristu ndiye mutu wa Mpingo, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo. 24Komatu


monga Mpingo amvera Khristu, koteronso akazi amvere amuna ao m'zinthu
zonse. 25 Akol. 3.19 Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda
Mpingo, nadzipereka yekha m'malo mwake; 26 Tit. 3.5 kuti akampatule,
atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau; 27 2Ako. 11.2 kuti Iye akadziikire

yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu


kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema. 28Koteronso amuna
azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa
iye yekha, adzikonda yekha; 29pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale
lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Khristu Mpingo; 30 Aro. 12.5 pakuti
tili ziwalo za thupi lake. 31 Gen. 2.24; Mrk. 10.7-8 Chifukwa cha ichi munthu

azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri
adzakhala thupi limodzi. 32Chinsinsi ichi nchachikulu; koma ndinena ine za
Khristu ndi Mpingo. 33 1Pet. 3.6 Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde

mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire
kuti aziopa mwamuna.

Aefeso 6

1  Miy. 23.22; Akol. 3.20 Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti
ichi nchabwino. 2 Eks. 20.12 Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo

loyamba lokhala nalo lonjezano), 3kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa
nthawi yaikulu padziko. 4 Deut. 6.7, 20, 24; Akol. 3.21 Ndipo atate inu,
musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha
Ambuye.
5  Akol. 3.22-24 Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa

thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukira
kanthu kena, monga kwa Khristu; 6 Akol. 3.22-24 si monga mwa ukapolo wa

pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu, akuchita


chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima; 7 Akol. 3.22-24 akuchita ukapolo

ndi kuvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye Yesu Khristu, si anthu


ai; 8 Akol. 3.22-24 podziwa kuti chinthu chokoma chilichonse yense achichita,
adzambwezera chomwechi Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu. 9 Aro.
2.11; Akol. 4.1 Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke

kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali m'Mwamba, ndipo palibe
tsankho kwa Iye.
Zida za Mulungu
10  Akol. 1.11 Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa
mphamvu yake. 11 2Ako. 6.7 Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze
kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. 12 Luk. 22.53; Aef. 2.2 Chifukwa

kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi
maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a
choipa m'zakumwamba. 13 2Ako. 10.4 Mwa ichi mudzitengere zida zonse za

Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita
zonse, mudzachilimika. 14 Yes. 11.5; 59.17 Chifukwa chake chilimikani,

mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha


chilungamo; 15 Yes. 52.7 ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a
Uthenga Wabwino wa mtendere; 16 1Yoh. 5.4 koposa zonse mutadzitengeranso
chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse
yoyaka moto ya woipayo. 17 Yes. 59.17; Aheb. 4.12 Mutengenso chisoti cha
chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu; 18 Akol. 4.2-4;
1Tim. 2.1 mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa

Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima


onse, 19 Akol. 4.2-4; 2Ate. 3.1 ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau

m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha


Uthenga Wabwino, 20 Akol. 4.2-4 chifukwa cha umene ndili mtumiki wa

m'unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula.


Tikiko apita naye kalatayo
21  Akol. 4.7 Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu

zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki


wokhulupirika mwa Ambuye; 22amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho,
kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. 23 1Pet.
5.14 Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro,

zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. 24Akhale nacho


chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka.

You might also like