Download as pdf or txt
Download as pdf or txt
You are on page 1of 2

NTHANO YA ANA (12TH AUGUST, 2023)

MALUWA NDI ANGELO


Melisa ndi mtsikana wachichepere amene
amakhala ku Poland. Ali tsitsi lokongola
kwambiri limene limafika cha m’mapewa mwake.
Ali ndi maso owoneka mwa brown amene
amadwala bwino akamasekerera. Akamapita ku
sukulu amakonda Kuvala chipewa cha mtundu wa
pink, jinzi ya blue komanso ma sokosi a pink
komanso pamodzi ndi zithunzi za agalu a mtundu
wakuda ndi woyera.
Mu njira monse, Melisa amaoneka mtsikana
wabwinobwino. Koma aphunzitsi ake amati
siwabwinobwino. Ndiwapadera. Izi ndi chifukwa
cha maloto amene adalota ali ndi zaka zisanu ndi
zitatu (8).
Mu malotomo, Melisa adagona pa kama ku nyumba. Pozungulira iye padali maluwa. Maluwa
osauma a mtundu oyera adali ku mutu kwake komanso ena chapamimba pake. Koma kenaka
maluwa aja adasitha. Cha m’musi mwa mimba yake kudali maluwa akuda komanso ouma. Maluwa
amenewa adali pa miyendo yake. Maluwa ena akuda koma oumanso adali ku mapazi ake.
Mngelo wina woipa adaima kumapazi ake kumene kudali maluwa a mtundu wakuda komanso
ouma. Iyeyu ankakangana ndi Mngelo wabwino amene adaima kumutu kwake kumene kudali
maluwa osauma.
“Mtsikanayu ndi wanga.” Mngelo woipa uja adatero.
“Iyayi, ameneyu ndi wanga,” Mngelo wabwino uja adayankhira.
Mngelo wabwino komanso mngelo woipa uja ankakangana kuti Melisa akhoza kukhala wandani.
Kenaka Melisa adadzuka.
Maloto amenewa akhoza kuoneka achilendo komanso oopsa kwa ana ena. Koma Melisa adalibe
nkhawa. Ku sukulu ankaphunzira za nkangano waukulu pakati pa Yesu ndi Satana. Iye ankadziwa
kuti pachiyambi Satana adali wabwinobwino amene ankakhala kumwamba. Koma kenaka Satana
adakhala mngelo woipa. Iye ankafuna kuti akhale Mulungu, ndipo adakopa angelo ambiri kukhala
mbali yake. Zimenezi zidayambitsa nkhondo kumwamba pakati pa Yesu ndi angelo ake abwino
kumbali imodzi komanso Satana pamodzi ndi angelo ake woipa mbali ina. Baibulo limatiuza za
nkhondo imene ndiyosaonekayi pa Aefeso 6:12, ndipo limati, “Chifukwa kulimbana kwathu
sitilimbana nawo mwazi ndi thupi, komatu nawo maukulu, ndi maulamuliro, ndi kuchita zolimbika
a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a choipa m’zakumwamba.” Angelo woipa akumenyana
ndi angelo abwino pa miyoyo ya atsikana komanso anyamata wokhala ku Poland komanso dziko
lonse. Nkhondo imeneyo idzatha Yesu akabwera ku dziko la pansi ndi kutenga owomboledwa
kupita nawo Kwawo kumwamba.
Loto lija silidamuchititse mantha Melisa chifukwa amadziwa kuti Yesu pamodzi ndi angelo ake
abwino samamumenyera chabe nkhondo komanso amamutetezera iye.
Melisa sadaliiwalebe loto lija, ndipo amakhala akuliganizira kawirikawiri. Iye akufuna akhale
wabwino komanso kupanga ziganizo zabwino. Iye akufuna kuti Yesu pamodzi ndi Angelo ake
abwino nthawi zonse adzikhala naye. Iye akufuna kuti Yesu komanso Angelo ake abwino akhale
wopambana kulikonse.
Tsiku lina ana ena ankakangana ku sukulu. Aphunzitsi adasokonezedwa maganizo ndipo
ankasowa chochita. “Ndingapange bwanji Pamenepa?” Aphunzitsi adafunsa ana amene
ankakangana aja.
Melisa adakumbukira loto lake lija. Angelo abwino komanso angelo woipa ankamenyana nkhondo
yosaoneka ku sukulu kwake. Angelo woipa ndi amene ankapangitsa kuti ana aja adzikangana.
Melisa adaimika nkono.
“Aphunzitsi, munatiuza kuti tikhale ndi mavuto, Tikhoza kupemphera,” Iye adatero.
Aphunzitsi adavomereza ndi mutu wawo. Iwo adaiwala langizo lawo lomwe limene adawapatsa
anawa. Lidali ganizo labwino kuti apemphera. Aphunzitsi aja adaitana ana onse pamodzi ndipo
adapemphera kwa Yesu komanso angelo ake abwino kuti apambane nkhondoyo. Akupemphera,
Satana komanso angelo ake woipa adagonjetsedwa. Yesu pamodzi ndi Angelo ake abwino
adapambana ndipo mtendere udabwerera nchimake pa sukulu paja.
Zikomo chifukwa cha zopereka za Sabata sukulu zimene zidathandizira ma sukulu apa kachisi ku
dziko lonse kufikira ana monga Melisa za chikondi cha Yesu.

WhatsApp: 0984589282/0884867782
Email: demobreyngwira2@gmail.com
FACEBOOK PAGE: Tell a Child with Uncle Demo

You might also like