Download as pdf or txt
Download as pdf or txt
You are on page 1of 36

CHICHEWA

KUZUKUTA

BUKHU
LA

NTHONDO
MAWU KWA APHUNZITSI NDI OPHUNZIRA

Bukhu la Nthondo ndi limodzi mwa mabukhu anayi omwe ali mu ndondomeko yatsopano
.Tebulo ili m’munsiyi ikusonyeza mabukuwa ndipo ayenera kuwerengedwa motere:

Form 3 Ntondo ndi kusintha maganizo ndi nkhani zina

Fomu 4 Kuyimba kwa mlakatuli ndi Chamdothi ndi zisudzo zina

Bukhu la Nthondo ndi la tinkhani (novel) ndipo choyamba ophunzira ayenera kudziwa zoyenera
kumaunika powerenga nkhaniyi (elements of novel) monga malo ndi nthawi komwe nkhaniyi
ichitikira (setting), atengambali (characters), mfundo zikuluzikulu (themes) ndi zina

M’bukhuli muli zina zofunika kwambiri monga zikhulupiliro za maloto, mankhwala azitsamba.

M’bukhu laNthondo mtengambali wamkulu ndi Nthondo amene mlembi wafuna kuonetsa kuipa
kwa makhalidwe oipa komanso ubwino wa makhalidwe abwino.

Nkhani ya Nthondo idachitika ku Nyasaland panthawi ya ulamuliro wa atsamunda. Malo oti


Kabula panopa amatchedwa Blantyre. Pa nthawiyi amene anali kulamulira anali azungu ndipo
anthu akuda ambiri adali osaphunzira. Nthondo atadwala ku Harare mutu waching’alang’ala
adatemera mankhwala achikuda koma adakana kuchipatala kuti akalandire mankhwala

achizungu. Mafumu atasonkhana pamene anabwera mzungu wofuna kukhazikitsa sukulu ku


dera la mfumu Chembe (atsibweni ake a Nthondo) anadabwa kuona wailesi. Iwo ankaganiza
kuti mu wailesi muli anthu omwe akuyankhula. Izi zikuonetsa umbuli omwe udamanga nthenje
pakati pa anthu makamaka chifukwa chosowa maphunziro.
MUTU 1 KUBADWA KWA NTHONDO

 Adabadwa usiku wozizira kwambiri bambo ake kulibe


 Bambo ake adatengedwa ndi asilikari
 Mayi ake a Nthondo adakondwa kwambiri chifukwa anali mwana yekhayo wamwamuna.
 Akazi onse m’mudzimo adapita kukaona Nthondo namusilira kukongola kwake.
 Anthu onse anakondwera naye Nthondo chifukwa cha kukongola kwake
 Amayi a Nthondo adatuma mnyamata kukauza abale a amuna awo zakubadwa kwa
Nthondo.
 M’mawa kudabwera anthu awiri kudzaona mwana. Anatenga ufa. Iwo anali mayi a
abambo ake a Nthondo ndi mlongo wawo.
ATENGAMBALI PA MUTU UMENEWU

1. Mayi ake a Nthondo.


2. Akazi onse m’mudzi wa Nthondo
3. Alongo ake a mayi a Nthondo
4. Mnyamata (nthumwi)
5. Mayi a abambo ake a Nthondo
6. Mwana wamkazi (mlongo wawo wa abambo a Nthondo)
MFUNDO ZIKULUZIKULU

1. Umodzi – akazi onse am’mudzi anapita kunyumba ya mayi ake a Nthondo kukaona
mwana
2. Chikondi –amayi awo a abambo ake a Nthondo ndi mwana wawo wamkazi anapita
kukaona matenda komanso mwana atauzidwa ndi mnyamata.
3. Kulimba mtima – mnyamata wokanena uthenga wa matenda anabwerera tsiku lomwe
ngakhale dzuwa linali litalowa.
4. Umphawi – kunalibe madzi oti aphikire phala loti amwetse mwana Nthondo
5. Kumvera – mnyamata atatumidwa kukanena uthenga kwa abale bambo ake a Nthondo
sanakane.
6. Nkanza – asilikari anawamanga abambo ake a Nthondo popanda chifukwa chenicheni.
ZIPANGIZO

1. Zining’a
(i) Kumbuyo kulibe maso
(ii) Chakudzas ichiyimba ng’oma
2. Mvekero
(i) Mphale vuuu! Tsuketsuke, phuu! Munsi tengu,
ZOLANKHULA ENA

(i) .”Mulungu wadziwa kusowa kwako pokupatsa mwana wamwamuna chifukwa


adzakutengera mabulangeti akakhala ndi moyo.”
a. Adanena mawuwa ndani?
b. Mawuwa adanena kwa yani?
c. Chifukwa chiyani mayi ake a Nthondo adakondwera kwambiri atabereka mwana
wamwamuna?
d. Chifukwa chiyani anthu onse anakondwera nayi Nthondo?
(ii) “Ine ndimafuna kudziwangati munakanena kwawo kwamwamuna uja za matenda a
mkazi wakeyu?”
a. Adanena mawuwa ndani?
Alongo ake a mayi ake a Nthondo

b. N’chifukwa chiyani mayi ake a Nthondo sanatumize uthenga kuchimuna?


Iwo ankaganiza kuti alongo awo atumiza kale uthengawo.

c. Kodi panthawiyi abambo ake a Nthondo anali kuti?


Anali atatengedwa ndi asilikari

(iii) “Ha! Mwana wakomadi. Mchombowu adatenga yani? Ife kwathuku makolo athu kulibe
wamchombo waukulu”
a. Adanena mawuwa ndani?
Mayi abambo ake a Nthondo

b. Anthuwa anali kuti panthawiyi?


Adali ali mnyumba kwawo kwa Nthondo

c. Ndi mphatso yanji yomwe adabweretsa?


Ufa
MUTU 2 : ATATE AKE A NTHONDO

ATENGAMBALI

1. Bambo ake a Nthondo


2. Asirikali

3. Kapitawo
4. Mwalapa
Adakokoloka ndimadzi pa mtsinjewina

5. A Dziko
 Adapha samba nthawi ya chirimwe bambo a Nthondo adapita kwa iwo

kukapempha matumbo a samba.


 Adauza bamboa Nthondo kuti akaphe ndiye mankhwala mmalo mwa matumbo a
samba omwe anali atatha panthawiyi

 Achikondi – adauza bambo a Nthondo kuti adye nawo nsima


6. M’balewa atate a Nthondo yemwe adavulazidwa ndi nyalugwe.
7. Mkamwini wa munthu wina
 Adaletsa bambo a Nthondo kuti asalime pena

8. Mchimwene wa mkazi wawo a bambo a Nthondo


9. Nkoswe zakuchikazi

10. Nkhoswe zakuchimuna


11. Waula
12. Adzukulu

13. Nthondo

MAKHALIDWE A ATENGAMBALI ENA

1. Kapitawo

 Wankhanza
 Waukali

Adakalipira bambo a Nthondo ndi ena omwe anagwidwa pamene amafunsa malo
ogona
2. Bambo a Nthondo

 Azikhulupiliro – adavutika ndi maloto – analota usiku atafika ku boma


3. Mayi a Nthondo
 Azikhulupiliro -
a. Adati usiku mwana analira kwambiri choncho bambo a Nthondo akapemphe
matumbo a samba

b. M,phala la mwana munalibe kachingwe ka mankhwala

MALOTO A BAMBO AKE A NTHONDO

Adalota atalembelera chulu ndipo atatsiriza kupanga litala, zinatuluka zochuluka. Anauza
mwana wawo wamkazi kuti auze amake kuti abwere ndimtsuko wodzatengeramo inswazo,

koma sanathe kuzimaliza.

Wina anati malotowa atanthauza mwayi. Ngakhale akuvutika tsiku lina adzamasulidwa.

ZIKHULUPILIRO PA MUTU 2

1. Zikhulupiliro za maloto

2. Zikhulupiliro za mankhwala
3. Mwana osayenda akamutengera paphewa amayamba kumera mano a mmwamba
chizindikiro choti ndi mfiti.
4. Zikhulupilro za maula – atadwala litsipa bambo ake a Nthondo ankhoswe akuchikazi ndi
akuchimuna adapita ku ula kuti akadziwe gwero la matenda ndipo ula udagwera mlongo

wina wa akazi awo a bambo ake a Nthondo.


5. Zikhulupiliro za mizimu – adakhwisula pa mtengo kuti mizimu yokwiya yomwe
yabweretsa matenda pa amuna awo a mai Nthondo ikhululuke ndikuchiza odwalayo.

6. Pochoka kumanda koika bambo a Nthondo adzukulu adagulula makasu ndipo adafika
kunyumba anatenga zinyatsi nawaula kuti azimu achoke.
7. Nthondo adamupatsa mkalo (dothi la kumanda) naponya mdzinje la manda kuti aiwale

msanga.
MFUNDO ZIKULUZIKULU PA MUTU 2

a. NKHANZA
 Kapitawo adakalipira omangidwa ndi asirikali
 Atsibweni ake a Nthondo amammenya kapena kumupha munthu akapanga
zosayenera kapena kuoneka ngati wawanyoza.

b. UMPHAWI
 Bambo a Nthondo adatuma mwana wawo kukapempha nkhuku zolipira
anamwino. Nkhuku zake zinafa ndi chideru.

 Bambo a Nthondo amagona mnyumba yansikidzi.


c. CHIKONDI
 Mnzake wadzina anamupatsa Nthondo nkhuku ndi ufa.
d. UMODZI

 Atamwalira bambo a Nthondo, anthu anabwera kudzalira ndikuika maliro.

MAFUNSO PA MUTU 2
1. Bambo aNthondo ankagwira ntchito yanji atatengedwa ndi asirikali?
2. Chidadzutsa mapiri pachigwa n’chiyani kuti bambo ake a Nthondo apatsidwe ntchito

mwatchulayo.
3. Tsimikizani popereka mfundo imodzi kuti kapitawo adali wankhanza.

4. Kodi maloto a chulu ndi inswa zambiri omwe bambo ake a Nthondo adalota
amatanthauzanji? Tsimikizani popereka mfundo imodzi.
5. Ndi makobidi angati omwe kapitawo adapereka kwa bambo ake a Nthondo atamaliza

kugwira ntchito?
6. Fotokozani mmene ndalamayo adayigwiritsira ntchito.
7. Kodi pamene asirikali amawatenga bambo a Nthondo adawapeza akuchita chiyani?
8. Tchulani zinthu ziwiri zomwe zikutsimikiza kuti makolo a Nthondo amakhala m’moyo
waumphawi.
9. Bambo a Nthondo nthawi ina anali ndi nkhuku zambiri pakhomo pawo.

10. Kodi m’manja mwa mwana ngati mukuzuna ndiye kuti akudwala nthenda yanji?
11. Tsimikizani popereka mfundo ziwiri kuti bambo a Nthondo sakadafa akadathamangira
nawo kuchipatala.

12. Tsimikizani kuti umbuli ndi zikhulupiliro ndi gwero la mikangano ndi imfa zina zopezeka
m’bukhuli. Lembani mfundo zinayi.

13. Kodi izi zimatanthauzanji?


a. Mwana akayamba kumera mano m’mwamba
b. Mukalandira chimanga chofiira

c. Olakwa akapereka mkanda woyera


14. Kodi mawu awa atanthauzanji
a. Kukhwisula

b. Chipindatchika
c. Mbuzi yakumitu
d. Mkalo

e. “kudulu”
15. “Ine ndine nkhalamba sindingakwatiwenso”
a. N’chifukwa chiyani mayi ake a Nthondo adanena mawuwa?
b. Mawuwa adanena kwa yani?

c. Fotokozani kuyipakwa mwambo wa chokolo.

d. Ndani amaganiziridwa kuti ndiye adapha bambo ake a Nthondo?


e. Tsimikizani kuti w aula yemwe ankhoswe adapitako adali wachinyengo.
MUTU 3 : UBWANA

 Nthondo adakula movutika chifukwa abambo ake omwe amapeza zosoweka


pakhomopo anamwalira.

i. Amasowa nkhuku
ii. Amasowa chimanga choti akonole

iii. Amasowa munthu oti awamangire nyumba kapena kuwakonzera tsindwi

lanyumba yawo likathyoka.


 Zomwe mayi a Nthondo amalingalira za amuna awo

i. Makhalidwe awo
ii. Mayankhulidwe awo
iii. Kusasowa kwawo
iv. Luso lawo

v. Anthu okamba nawo.


vi. Kukondana kwawo
 Malingaliro adawachititsa mayi ake a Nthondo:
i. Kuyamba kuonda
ii. Kukhala osasangalala.
 Zomwe mayi a Nthondo adachita atasowa owamangira nyumba itapsa ndi moto
i. Adapita kwa bwenzi wawo kukapempha chimera kuti afulule mowa
ii. Adakapempha chimanga kwa alongo (achimwene) awo.
iii. Adafulula mowa koma udali pang’ono.
ZOTSATIRA

Nyumba sinamangidwe popeza mowa unatha ndi kalawe komanso kugulana.

a. Anthu ena amakatema nsichi


b. Ena kumweta udzu
c. Ena kukafuna phaso lake

Mowa utatha anthu anabalalika asanamange nyumbayo. Munthu wina ataona izi anamva
chisoni natsirizitsa.

MAKHALIDWE OIPA A NTHONDO

a. WABODZA
i. Pamene nyumba inapsa mayi ake anamuuza Nthondo kuti awamangire tsindwi
koma iye anangovomera koma sanamange. (p27)
ii. Pamene wina anamudzudzula Nthondo posamangira mayi ake nyumba iye

adanama kuti amamva litsipa (p29)

iii. Atsibweni a Nthondo atamufunsa Nthondo za nkhunda zomwe iye anaba,


Nthondo anakana nauza atsibweni ake wo kuti iye sanabe koma kuti iye
amangopita pafupi ndi chikukumba cha nkhundacho. Apa mwini wake anayamba

kufuula kuti iye wawaber. Koma tsiku la mlandu iye sanatsutse zoti iye anaba.
iv. Nthondo ananena bodza powuza mayi ake kuti amasewera pamene

anamufunsa za kutuwa kwake (p24). Choona chinali choti amamenyana ndi


anzake kuubusa.
v. Nthondo atauzidwa kuti akadulemtengo aseme mpini, iye sanapite. Mmawa

mwake Nthondo adanena bodza pouza atsibweni ake kuti ena ake
anamupempha kuti akawasosolere nkhuku (pg33). Apa atsibweni akewo
anatenga mtengo namuthamangitsa kuti ammenye.
vi. Nthondo adanena bodza pouza atsibweni ake kuti iye anasiy mayi ake
akudwalabe pamene iye amapita kwa mnzake wadzina. Ilitu linali bodza popeza
iwo anayamba kudwala Nthondo atathawira kwa mbzake wadzinayo atapalamula

kwawo.
vii. Nthondo adanena bodza atapalamula kwaa Mdima pamene adalephera
kuthandiza kumanga tsindwi la nkhokwe ponena kuti iye akudwala ntchofu.

Anzake ena aja anathandiza nawo.


b. WAKUBA

i. Nthondo adayamba kuba ndiwo, mazira ndi zina za mnyumba mwa amake
pokhumbira zimene anzake amadya kumphala. Ali kumphala Nthondo
adaperekeza anzakewo kokaba misinde koma iye samadya nawo. Amaona

nkhuku zobedwa zikuotchedwa koma iye samadya nawo poopa kuti angalumale.
ii. Nthondo adaba zipwete kumunda kumene amasaka mbewa. Mwini zipwete
anamuona koma iyeanathawira pa tchire osamugwiranso.

iii. Mmawa mwake Nthhondo anaba nkhunda ndipo eni ake anamuthamangitsa
namugwira. Anthu adamumenya Nthondo namuikira nthenga za nkhunda mtsitsi
lake nayamba kuyimba nyimbo uku akupita naye kwawo. Atsibweni ake analipira

mbuzi zisanu powombola Nthondoyo.


iv. Nthondo anakaba misinde usiku ndipo anachita kawirikawiri. Mwini wake
anachenjeza ndi kuopseza kuti aliyense wopezeka akuba m’mundamo amulasa.
v. Nthondo adaba mbota pamene adapita kwa mnyamata uja adabwera kuchokera

ku Harare. Iye adaipotapota mbotayo tizingwe totchelera mbalame.

vi. Nthondo adaba thumba lachikopa chambuzi kuti akaikemo ufa (pg39)
vii. Nthondo adaba ufa omwe udayanikidwa pa dzuwa nakaubisa ku phanga kuti
azikadya popita ku Harare. (pg39). Ufawo anakawusiya kwa mnyamata

adabwera ku Harare uja.


c. WOUMA MTIMA/WOPANDA CHISONI

i. Ngakhale adadziwa kuti nkhuku yomwe anzake adaba idali yamayi ake, Nthondo
sadaulule. Amake adadandaula kusowa kwa nkhuku yawo komaiye sadamve
chisoni.adaumitsa mtima pofuna kukondweretsa anzakewo.

ii. Nthondo adagenda ndi mwala alendo omwe amafunsa njira. Atanena kwa a
mfumu alendowo adalephera kuloza yemwe adawagenda poti sanamudziwe.
Amfumu adati amafuna amulipiritse ogendayo.
iii. Amake a Nthondo adadandaulira Nthondo kuti amange nyumba yomwe idapsa
ndimoto komaiye anangovomera koma sanamange.
iv. Nthondo atawuzidwa zakudwala kwamayi ake ndi munthu yemwe anatenga

thumba la nyemba, iye sanalabadire zamatendawo, sanauzenso mnzake


wadzina uja za matendampaka adamwalira.
v. Nthondo sadamvechisoni ngakale amfumu adadandaula zakubedwa kwa ufa uja.

Iye adaumitsa mtima ngakhale amfumu anati ana awo afa ndinjala chifukwa
chakubedwa kwa ufawo (pg39)

d. WOSAMVERA
i. Nthondo sadamvere mayi ake atamupempha kuti awamangire nyumba. (pg27)
ii. Nthondo anakalipira munthu yemwe adamulangiza kuti awamangire amake

nyumba pomuuza kuti iye safuna kulangizidwa.


iii. Mayi ake atamuchenjeza za kuipa kwa kuba komanso chenjezo loti wakuba
misinde adzalasidwa iye sanamvere. Adamkakamiza mnzake kukaba ndipo

mnzakeyo analasidwa nafa.


iv. Asanamwalire abambo ake a Nthondo anamulangiza kuti “Nthondo ine ndikufa.
Mwanawe leka magwiragwira chifukwa amapha manja; mapenyapenya

amaphamaso.” Koma atamwalira Nthondo sanamvere malangizowa. Iye amaba


zinthu zosiyanasiyana za eni mongankhunda, mbota ndi zomwe
zinamupezetsamavuto.
v. Atsibweni ake anamuuza kukafuna mtengo kuti aseme mpini koma Nthondo

sanamvere. Iye anapita kukasewera ndi anzake.

MAKHALIDWE ENA A MPANGANKHANI

a. NTHONDO

i. WACHISONI
 Nthawi zina Nthondoo amakana nsima amake akampatsa poona kuti amake
sakusangalala pamene abambo a Nthondo anamwalira. Amake akamufunsa
amangoti kukhosi kwake kwada.
ii. WAMANTHA
 Pamene Nthondo adatsatira anzake kukaba misinde, iye amatsalira m’mbuyo kuti
eni ake akawagwira adzakane kuti iyesamaba nawo.
 Iye samadya nawo nkhuku zakuba kuopa kulumala poti panthhawiyo kunali chambu
b. MAYI AKE A NTHONDO
i. Achikondi
 Adachenjeza mwana wawo Nthondo kuti asayerekeze kukaba misinde malinga kuti
kutero akalasidwa.
 Amake a Nthondo akaona chakudya amatemera Nthondo naye Nthondo akapeza
amatemera mayi ake (p21)
 Amake a Nthondo sanamuzenge mlandu pamene mwana wina anatentha nyumba
yawo chifukwa analimwana wapamodzimodzi pomwepo. Iwo adatero polinga
mawa.

Koma mawalo ena anawamvera chifundo?


AYI : Nthondo ataba khunda atsibweni ake adalamulidwa kulipira mbuzi zisanu ndi
eni nkhundazo
EYA: Wina pomvera amake Nthondo chisoni adamaliza kuwamangira nyumba
ii. Anzeru
Adakana kuti m’bale wa mwamunawawo awakwatire atamwalira amuna awo

ponena kuti iwo ndi nkhalamba sangakwatiwenso (pg 20)

ZOMWE NTHONDO ADAPHUNZIRA

a. KU MPHALA
i. Kuba – anzake a Nthondo amamjutenga pamene amapita kukaba zinthu
zosiyanasiyana monga misinde
ii. Kupilira – ngakhale ku mphala kunali mphutsi, Nthondo anapilira nazo.
iii. Kusunga chinsinsi –iye sananene kwa mayi ake ataona nkhuku yawo itabedwa
ndi kuphedwa ndi anzake ku mphala.
b. KU UBUSA
i. Kupilira – ngakhale amauzidwa kuchita ndeu ndi wina, iye sanaleke kupita ku
ubusa.
ii. Kutumika – mtsogoleri akawauza kuchita chinthu iwo samawilingula, amachita
chinthucho. Mtsogoleri amawauza kuchita zinthu monga kuchita ndewu popanda
kuyambana kapena amawuza kubusa mbuzi.
iii. Ndewu – mtsogoleri akawauza kuchita ndewu ndi wina popanda kuyambana
ndipo amamenyanadi
iv. Kulimba mtima – chifukwa cha ndewu yomwe anyamatawa ankachita kuubusa,
iwo adaphunzira kulimba mtima.
MFUNDO ZIKULUZIKULU PA MUTU 3
1. KUBA
Nthondo adalowerera nayamba kuba zinthu za mayi ake komanso za eni. Iye adaphetsa

mnzake pamene adalasidwa akubamisinde.


2. UMODZI
Nthondo adaphunzira kuchita zinthu pamodzi ndi wena

3. KUPIRIRA
Kupilira kwaonetsedwa ndi anyamata a kumphala omwe mnyumba ngakhale

mulimphutsi zimawaluma.
4. UMPHAWI
Anyamata ku mphala amagona mwaumphawi poti mphutsi zimawaluma.

ZOYANKHULA ZA ATENGAMBALI ENA (QUOTATIONS)

1. “Nanga muno ukutulukiranji?”

“Iyayi, sindifuna ine chifukwa anzanga angamandiseke kuti ndine munthu wogona
m’kuka”.
a. Tchhulani anthu awiri omwe akuyankhulana mkankhanika.
Nthondo ndi mayi ake
b. Tchulani makhalidwe abwino awiri omwe Nthondo adaphunzira ku mphala
Kutumika ndi kupilira
c. Ndi chiyani chomweNthondo amakhumbira kumphala kuja?

Kuweta mbuzi
d. Kodi mtsogleri amamusankha bwanji ku ubusa?
Abusa amenyana ndipo yemwe amaposa ena amakhala mtsogoleri.
2. “Masulani mbuzi, lero ndikaziweta ndine.”
a. Nthondo amayankhula kwa yani?

b. Chifukwa chiyani mbuzizi adazimanga?


c. Tchulani makhalidwe oipa awiri omwe Nthondo adaphunzira ku mphala
3. “Ine sindifuna wina andiweruze”

a. Ndi khalidwe lanji lomwe Nthondo waonetsa?


Wosamvera/wamakani
b. Nthondo adatani ndi munthu amamulangiza?
Adamenyana naye
c. Fotokzani mwachidule malangizo omwe munthuyo amapereka kwa Nthondo.
Iye adamuwuza Nthondo kuti amayi ake sayenera kuvutika iye alipo. Iye anayenera
kuwamangira nyumba.
4. Tchulani makhalidwe auchigawenga a Nthondo.
 Nthondo adagenda alendo omwe amafunsira njira ndipo m’modzi adavulala
 Akakumana ndi ana a m’mudzi wina ku nsanga (kutchire) amawapitikitsa
5. Chifukwa chiyani Nthondo samakonda kukhala pamudzi?

 Amaopa akulu kumutuma


 Chifukwa cha khalidwe lakeloipa
6. Kodi azungu adali pa mudzi wa yani?

 A Msinda
7. “Dzulo lija ndinachedwa chifukwa auje adandituma kuti ndikawasosolere nkhuku.”
a. Kodi Nthondo ankayankhula ndi yani?

b. Nthondo adauzidwa kuchitachiyani?


c. “Ndiwe mwana woipa ukana zomwe ndikutuma ine osakhhala ngati udaonongetsa
mbuzi zanga zisanu………”.

i. Kodi mbuzi zisanu zinaonongeka bwanji ndi Nthondo?


Adalipira mlandu wa nkhunda zomwe Nthondo adaba
ii. Kodi Nthondo atathamangitsidwa pakhomopa adapita kuti?
Kwa mzake wadzina
8. Tsimikizani kuti woipa athawa yekha malingana ndinkhaniyi.

9. “Kukadakhala kufupi ndi kwathu ndikadadzaba chumachi.”


a. Adali kuti Nthondo panthawiyi?
Kwa mnyamata yemwe adabwera kuchokera ku Harare
b. Tchulani chuma chimene adaonetsedwa kumeneko.
Sopo, thaulo, mipeni
c. Ndi chiyani chimene Nthondo adaba kumeneko?
Mbota
10. Nthondo ankafuna kupita ndi yani ku Harare?

A Mdima
11. “Ine sindikakonza nawo chifukwa ntchofu yandivuta kwambiri.”
a. Anzake a Nthondo ankagwira ntchito yanji?
Yokonza tsindwi la nkhokwe
b. Ndi khalidwe lanji Nthondo waonetsa pamenepa?
Waulesi, wachinyengo. Adanena bodza kuti akudwala ntchofu pozemba ntchito.
MUTU 4 : MAULENDO AKE

MAVUTO OMWE ADAKUMANA NAWO PAULENDO WA KU HARARE

a. MATENDA
Mnyamata wina adamva litsipa pa Dzalanyama (p42). Anzake adafuna kangaluche

namutentha nasakaniza ndi tsabola namutemera wodwalayo koma sanachire.


b. MAKANGANO

Anzake a Nthondo anamuuikira namumenya chifukwa cha ulesi wake. Iye adakakana

kukagwira ntchito pamudzi wina kuti apeze chimanga. Iye adanama nati dzanja lake
likuwawa.
c. KUSOWA CHAKUDYA

Chifukwa chakutalika kwa ulendo, matumba awiri omwe adapatsidwa atagwira ntchito
pamudzi uja chidawathera ndipo ankadya maswu (p43). Onse anayamba kuwonda ndi
njala moti pamene amaoloka Zambezi nkuti ali mafupa okhaokha.
d. KUTALIKA KWA ULENDO
Ulendo wawo udali wautali kotero kuti adayenda masiku ambiri ndipo pamene amafika

anali otopa kwambiri.


e. KUGWIDWA KWA NTHONDO
Nthondo adapita pamudzi wina kukaba mapira ndipo mwini wake atamugwira

anamenyedwa koopsa. Kenaka analamulidwa kugwira ntchito kwa chaka chimodzi


pakhomopo ngati chilango. Nthondo adathaw atabanso chimanga pakhomopo napitirira
kupita ku ulendo uja. Adakumana ndi gulu lina nawanamiza kuti anzake anamusiya

akudwala.

NTHONDO AKUMANA NDI ANZAKE KU HARARE , APEZA NTCHITO KWA


MZUNGU
Nthondo atafika ku Harare adapeza anzake akugwira ntchito yosesa kwa mzungu.

Chifukwa cha mantha iye adakana kufunsa ntchito kwa mzungu yemwe anzake
anamuuza kotero kuti wina anachoka naye napita naye napeza ntchito yoweta nkhuku.

Pantchitoyi Nthondo ankachita izi:


i. Kupatsira nkhuku madzi
ii. Kupatsira chakudya

iii. Kusonkhanitsa mazira.


Mzunguyo ankapatsa Nthondo ndalama khumi ngati malipiro ake.

MAKHALIDWE A NTHONDO KU HARARE

a. WANZERU

Nthondo adaonetsa khalidweli pogwiritsa ntchito bwino malipiro ake. Iye adagula
bulangeti ndipo zina anasunga.

b. WAKUBA

Nthondo adaonetsa khalidweli popita kukaba maungu atatu m’munda mwa mzungu.
Mwatsoka mlonda adamugwira nampereka kwa mzungu wake. Mzungu analemba

kalata yopita kuboma. Msilikari anabwra namumangirira Nthondo kumimba kwa


kavalo napita naye ku ndende komwe adakakhalako masabata atatu. Kundendeko
Nthondo amadya nsima yosakaniza ndi mchere.
Atatha masabata atatu aja mzungu uja anammenya zikoti zinayi , namtulutsa.

MALOTO A NTHONDO KU NDENDE


Nthondo adalota atalowa mdziko la mdima. Mnyamata wina amene kale analasidwa
kumunda uja adayamba kumuthamangitsa, koma samaonetsetsa chifukwa cha
mdima uja. Adangoona kuti mano ake asanduka aatali. Nthondo adayesa kuthawa
koma mnzakeyo sadamuleke. Nthondo adadzidzimuka ndi mantha ambiri.
c. Wabodza
 Nthondo adaonetsa khalidweli ponamiza anzake kuti akudwala ndipo sapita
ku ntchito koma ali ndi malingaliro oti apite kokaba maungu m’munda mwa
mzungu wake.
 Nthndo adaonetsanso khalidweli ponamiza mzungu wake kuti nkhuku imodzi
idasowa pomwe adachita kuipha. Mzungu adamkhulupilira nanena kuti

palibe kanthu.

NTCHITO ACHOTSEDWA NTCHITO YOWETA NKHUKU

Atatulitsidwa kugadi Nthondo adapita kwa bwana wake ndi cholinga choti akapitirizenso ntchito.
Kodi Nthondo adakumana ndi zotani?

a. Nthondo adapeza kuti wina watsegulira kale nkhuku zija.


b. Mzungu adaitana agalu ake kunyumba kumupitikitsa Nthondo.

c. Akuthawa anapunthwa ndipo galu wina anamuluma pamsolo.


d. Mzungu ua anamulanditsa kwa agalu aja koma sanasiyire pomwepo koma
anayambanso kummenya makofi. Iye ananyamuka kupita komwe amakhala nayamba
kulira.

NTHONDO APEZA NTCHITO INA: MTSOGOLERI WA NGOLO

 Ngolo imakoka ndowe yothira mmunda


 Anagwira ntchito chaka chimodzi
 Pamene anapeza ndalama anagula zovala ndi bulangeti.

 Tsiku lina mmawa pamene munthu wofulumiza ng’ombe amazimenya, chingwe


chidaphuluza ndi kumenya khutu la Nthondo. Pomwepo Nthondo adataya chingwe cha

ng’ombe ndikududukira mnzakeyo namuluma chala. Akulimbana Ntondo adamponda


mnzakeyo pamtima nakomoka.
 Mzungu wagadi adamuweruza kuti akhale ku ndende miyezi isanu ndi umodzi poti

mnzakeyo sadafe. Iye adati akadafa mnzakeyo ndiye kuti nayenso akanaphedwa.
MALOTO ENA A NTHONDO KUNDENDE
a. Iye adalota atapita ku uzimba ndi anzake ndipo mikango iwiri imamuthamangitsa,
nimugwira nikumudya. Atadzuka Nthondo adayamba kulingilira kuti mwina panali wina
amene adamuchitira mankhwala kuti azichimwa popeza anzake amakhala
mwamtendere.

b. Tsiku lina adalota munthu wina amene adavala nsalu zoyera adali ndi ndodo yowala
ndipo adamuloza ndi ndodo yakeyo ndi kuti: “Ndizakulanga ukapanda kusiya zoipa
zakozi”. Pamene adadzidzimuka adayamba kusisima chifukwa camaloto amenewa.

ZIKHULUPILIRO
i. Nthondo adakhulupilira kuti maloto omwe adalota amatanthauza kuti amfiti

akumutambira
ii. Nthondo amakhulupilira za umfiti. Iye adanamiza anzake tsiku lina kuti akudwala
napita kwa sing’anga kuti akampatse mankhwala a thupi kuti mfiti zisamafike

pakhomo pake.
Ndoda ija idamuwuzanso nthondo za mankhwala a liphopho, mankwala a mdima
ndi mchira wafisi kuti azikabera. Iye adampatsa sing’angayo ndalama khumi ndi

zisanu.
NTHONDO ABWERERA KWAWO
 Nthondo adanamiza mzungu wake pomuuza kuti m’bale wake wamwalira pofuna kuti

amulole kuti apite. Iye anamuuza Nthondo kuti adzabwerere kukapitiriza ntchito.
 Atauza anzake aja anamukanira nati iwo apitabe mtsogolo.
 Ananyamuka ndi anthu oyandikira kwawo koma anasiyana pamudzi wina pamene iwo
anamuukira Nthondo kuti amasekachomwe samachidziwa. Nthondo adawauza kuti

pamudzipo ndi pomwe iye adamangidwa ataba mapira.

 Mnjira wina anati amulandire katundu poti amaoneka otopa. Atampatsa katunduyo
munthuyo anamubera pamene iye amachotsa thekenya ndikumwa madzi kumtsinje.
 Atafika kunyumba atsibweni ake anamulandira. Anapereka nkhuku kwa anyamatawo

pofika naye nthondo.


 En anamunyoza chifukwa cha usiwa.

 Nthondo udaganiza zaupandu chifukwa chotopa ndi kusekedwa ndi anthu. Adapita kwa
munthu yemwe anabwera ku Harare nakaotcha nyumba. Popita akaone motowo, iye
anakaba chuma chake.

NTHONDO APHUNZIRA LUSO LOYIMBA; ALANDIRA MPHATSO


 Nthondo adaphunzira luso lokonza ming’oma ndi kuimba ndi nsasa. Kuimbaku
kunamupindulira moti anthu ambiri amabwera kudzamumvera.
 Ena amamuchitira nsanje. Tsiku lina iye anapita kumowa wammeto. Kumeneko
adapatsidwa nkuku, mbuzi ndi nkosa. Ziwetozi adasiya kwa atsibweni ake aja.
NHONDO NDI ANZAKE ASAUKANSO : AKONZA ULENDO WOPITA KU KAPATA

1. Mtsogoleri paulendowu anali Nthondo popeza anali wokula msinkhu uposa anyamata
onse.
2. Iwo ankafuna kukatenga katundu ku Kapata kukatola ku Kabula.

3. Iwo anamva kuti ntchito yamtengatenga munthu amapatsidwa ndalama khumi ndi
zisanu.

4. Iwo sanafune kubwerera ku Harare chifukwa anali atangobwrera kumene moti


akuluakulu sakadawalola kutero. Nthondo adauzidwanso kuti mnyamata yemwe
adammenya uja adamwalira kotero kuti mwina akadafikira kuzengedwa mlandu.

MAVUTO OMWE ADAKUMANA NAWO PA ULENDO WOPITA KU KAPATA


a. Kutalika kwa ulendo. Iwo adayenda mtunda wotalika moti miyendo idatupa.
b. Nthawi zina ankayenda msanga mokhamokha momwe amachita mantha ndi nyama

zamtchire monga ntchefu, mphalapala, akatenthe ndi mbawala. Adaonanso matakadzo


a mikang, afisi komanso maenje a njovu zomwe zimawachititsa mantha.
c. Kawolokedwa kamtsinje wa Buwa. Iwo adauzidwa za kuopsa kooloka Buwa ngati palibe

mtsogoleri.
d. Nthondo adakola pamsampha wanjira pamene amathawa kugwiridwa pamene amati
akabe nkhuni pakhomo pa munthu wina. Nthondo adamenyedwa kwambiri
nammangirira ku mzati wa nkhosa. Nthondo adamulipitsa napitilira mpaka kukafika ku

Kapata.

ZABWINO ZOMWE NTHONDO NDI ANZAKE ADAONA POPITA KU


KAPATA
1. Adaona mitengo yambiri yongoti see! Adaikhumbira poti kwawo amayenda mtunda

kuti akapeze nsichi yosalala.


2. Adaona mudzi omwe munali dulitsedulitse wa mipanda. Zipata zake zinali zambiri.

Unali mudzi wabwino. Munali mitengo yambiri yamitawa, anyamata ndi asungwana
ambiri.
3. Adakaonerera gule wa ngoma pamudzi wina omwe adagona. Nthondo adavina

guleyo.
4. Adaona udzu omera pamwamba pamadzi. Udzu umenewu umatchedwa Gumbwa
omwe adachita nawo chidwi.

Atafika ku Kapata mzungu wina adawapatsa thonje ndi kalata yokaperekera katunduyo.

MALOTO A NTHONDO KU KAPATA

Adalota ataona atate ake amene adafa kale akupha nsomba ndipo Nthondo adapemphako,

koma atate ake adamukanira namuuza kuti si iyenso mwana wawo popeza akuwachititsa
manyazi ndi kuba kwakeko. Pamenepo Nthondo mosadziwika anabako nsomba imodzi. Atatero
atate ake adayamba kumpitikitsa. Nthondo adayesetsa kuthawa ndi kuuluka koma osatheka

mpaka atate ake adamugwira pakhosi nabanika.

Matanthauzo a maloto a Nthondo

Wina anammasulira kuti munthu amene alota munthu wakufa nziwanda.

Chithandizo

Anamuwuza kuti azisamba mankhwala aziwanda kuti asadzapenge mtsogolo mwake. Ena
anamuuza kuti akakumbe mtengo wamathulitsa ena amati chivumulo.

ULENDO WA KU KABULA

 Ataoloka Buwa kuchokera ku Kapata adasintha njira natenga yachidule.


 Adaona mpembe wa njovu ndipo anabwerera nagona pakhomo pena.
 Mnyamata wina miyendo imamupweteka ndipo adagwirizana kuti apume asapitirire.
Adaona mmbulu ikugwira mbawala. Adapangana nalanditsa natenga mbawalayo

nkuiwotca. Chifukwa chodyetsa Nthondo adatsegula m’mimba. Adakhalabe pamudzipo

kuti Nthondo achier. Nthondo adachira koma winayo sadachirebe. Adakhalabe mpaka
tsiku la Sabata.
 Chisanu chitawavuta anapita kukaothera dzuwa komwe adamva beru kuti nge! Nge!

Nge! nge! Atafunsa anauzidwa kuti linali tsiku lopita kukapemphera ku tchalitchi
kukapembedza Mulungu.

 Nthondo ndi anzake adapita nawo ku tchalitchi komwe iye adasilira nyimbo zomwe
zinkaimbidwa. Iye adati akadakhala kwawo bwenzi akuimbira nsasi.
 Kutchalitchiko Nthondo adamva ulaliki omwe udamukhudza kwambiri. Mphunzitsiyo

adati onse ochita zoipa monga kuba, dama, kupha, ndi zina sadzalowa mu ufumu wa
Mulungu. Iye adamva chisoni chifukwa mwini kba, dama ndi kupha adali iyeyo.
 Nthondo adakhumbira sukulu.

NTHONDO ATEMBENUKA MTIMA

“……………..koma ngakhale ndipite kwathu kuba ndi zina ndaleka lero. “adatero Nthondo
pamaso pa anzake aja polengeza za kulapa kwake. Izi anachita potsatira ulaliki omwe adamva
ku tchalitchi kuja.

MALOTO A NTHONDO

Nthondo adalota akupita kudziko lachilendo. Kumeneko adapeza anthu akunzunzika ndi moto
wophulitsa maso ndipo anthu ena anali kuyimba nyimbo zonga zomwe zakutchalitchi kuja.

Kugulu lakumotolo kunali munthu woopsa wanyanga ziwiri ndi mchira. Kugulu linali kunali
munthu wamtali wovala zoyera. Anthu awiri amene anali atsogoleri anayamba kumulimbirana

Nthondo atafika. Mtsogoleri wakumotoyo anamkumbatira pamimba namkokera kumoto


pamene wabwinoyo adangogwira dzanja. Atalimbirana Nthondo adauka.

NTHONDO NDI ANZAKE AFIKA KU KAPATA

Nthondo ndi anzake aja adafika ku Kapata nasiya katunduyo kwa mzungu uja. Adafotokozera
mzungu chifukwa chomwe adachedwera mu msewu ndipo adawapatsa ndalama zawo napita

kwawo. Iwo adayenda usana ndi usiku pa ulendo wopita kwawoko.


ZOYANKHULIDWA NDI ATENGAMBALI ENA

1. “Komai ne ndidziwa kuti mnyamata wina anandinenera kwa mzungu wanga kuti
asandilandirenso chifukwa masiku onse ngakhale nimagwira ntchito samandiona ndi
maso abwino. Chilipochilipo paja galu wa mkota sakandira padzenje lopanda kanthu.”
a. Ndi ntchito yanji yomwe Nthondo amagwira kwa mzungu amaneyu?

Ntchito yoweta nkhuku


b. Tsimikizani kuti nankununkha sadzimva maling ndi zomwe zidamuchitikira Nthondo.

Nthondo adaleka kuvomera mumtima mwake kuti khalidwe lake lakuba ndi lomwe
lamuchotsetsa ntchito koma adayamba kudzudzula anzake ogwira nawo ntchito pa
kuchotsedwa kwake.
c. Chifukwa chiyani mzungu wa Nthondo sadamulandirenso Nthondo atabwera kugadi?
Iye samafuna munthu wakuba pakhomo pake
d. Nthondo adakhala kugadiko nthhawi yotalika bwanji?
Masabata atatu
e. Ndi nkhanza zanji zomwe adamuchitira kundende?
Anammenya zikoti zinayi
f. Fotokozani zomwe zidamuchitikira Nthondo atafika kwa bwana wake kuti
ayambenso ntchito.
Mzungu adaitana agalu ake nayamba kumupitikitsa Nthondo. Akuthawa adapunthwa
ndipo galu wina adamuluma pa msolo. Mzungu uja anamulanditsa kwa agalu aja
koma sanasiyire pomwepo koma anayambanso kummenya makofi. Iye adanyamuka
kupita komwe amakhala nayamba kulira.
g. Perekani matanthauzo a ziganizo izi:
i. Samandiona ndi maso abwino

Samasangalala nane
ii. Galu wamkota sakandira padzenje lopanda kanthu
Zinthu zina zikamachitika zimalosera zovuta zochitika mtsogolo
2. “Mukaona zii ndiye kuti ndagwiridwanso chifukwa ndine munthu watsoka.”

a. Ndani adanena mawu amenewa?


Nthondo
b. Munthu anapita kuti panthawiyi?

Iye amapita kukafuna ntchito


3. “Iwe ndiwe yani?”
“Ndine Nthondo bwana.”
“Ukufuna chiyani?”
“Ndikufuna ntchito”

“Kale umagwira kuti ntchito?”

“Sindinagwireko ine ntchito koma ndikuchokera kumudzi”


a. Ndi ntchito yanji yomwe Nthondo adapeza kwa mzunguyo?
Kukhala mtsogoleri wangolo yonyamula ndowe
b. Chhifukwa chiyani Nthondo adanena bodza kuti sanagwireko ntchito kumalowa?
Iye adafuna kubisa mbiri yake yoipa popeza anamangidwa atamubera bwana wake
maungu atatu kumunda wake.
c. Kodi Nthondo anakakhala nthawi yayitali bwanji kugadi atpezeka wolakwa atakomola
mnzake?

Miyezi isanu ndi umodziv


d. Fotokozani maloto a Nthondo ali kugadiko.
Iye adalota atapita ku uzimba ndi anzake ndipo mikango iwiri imamuthamagitsa
nimugwira ndi kumudya. Atadzuka Nthondo adayamba kulingilira kuti mwina panali
wina amene adamuchitira mankhwala kuti azichimwa popeza anzake amakhala
mwamtendere.
4. “Ine ndisagonetse m’dziko lino. Kuno ndingangoferako chifukwa ndavutika kwambiri.
Ndichoke.”
a. Kodi Nthndo amadwala matenda anji?

Litsipa laching’alang’ala
b. Kodi Nthondo amatanthauzanji ponena kuti “ine ndisagonetse m’dziko lino”?

Ine ndisakhalitse/ndisatchone mdziko lino


c. Mnyamatayo adammenya Nthondo khofu ….”Chifukwa chiyani Nthondo
adamenyedwa?

Nthondo amakana kumwa mankhwala choncho amamukakamiza kuti amwe.


d. Ndi zoopsa zanji Nthondo akadakumana nazo kupanda kubwerera kwawo pa
nthawiyi?

Nthondo akadamangidwanso chifukwa choti munthu adamkomola uja adamwalira.


5. “Tafika ife a Mataya osasamala ndalama. Mukaigwiritsa ndalamayo idzaswa kdi?
Ndalama nza azungu, ife tingosauka.

a. Kodi Mataya ndani?


Nthondo
b. Perekani mfundo imodzi yotsimikiza kuti munthuyi ndi Matayadi.
Iye amagula zakudya mosaumila yekha ndikumadya ndianzake.
c. Kodi amayankhula kwa yani?

Iye amayankhula kwa anzake paulendo wopita kwawo kuchokera ku Harare


d. Munthuyi adali kuti panthawiyi?
Iye anali paulendo wopita kwawo kuchokera ku Harare.
6. “Moni amunanga.”
“Eya waphika ndiwo zanji lero?"

“Ndikaphika ndiwo zotani pomweiwe nyama ukungodya wekha osakumbuka mkazi


wako?’
a. Tchulani anthu awiri akuyankhulana nkankhanika.

Mdzitula ndi Nthondo


b. Anthuwa ali kuti?
Akumana kumunda
c. Pali ubalewanji pa anthu awiriwa?
Mdzitula ndi msuweni wake wa Nthondo
7. “Ha! Ndani angabere ine Nthondo mwana wa a Kumphepo, wobadwa fisi nalira.

Amanama amene amateroyo”


a. Ndi khalidwe lanji Nthondo waonetsa pamenepa?
Wamatama
b. Nthondo ankayankhula ndi yani?
Mdzitula
c. Chifukwachiyani Nthondo amakana kuti sanaberedwe chuma chake?
 Samafuna kuoneka opusa pamaso pa msuweni wakeyo.
 Iye anali ali ndi malingaliro ofuna kukaba chuma kwa mnzake anabwera ku
Harare pofuna kuti anthu aziti chinali chuma chake.
8. “Ha! Ku Harare kusamakhala ngati kumene adanka a Nthondo komukira nkhuli.
Ndikadakhala ine ndikanapitanso ngati, ha! Iyayi. Ndiko kongotsata imfa.

a. Chifukwa chiyani mnzakewa Nthondo adayankhula mawuwa?


Nthondo adavala nsaza zomatika ndi zikumba zaakunda (bwampini) asanu omwe
adapha.
b. Usiwa wa Nthondo udachepa bwanji panthawiyi?
Anzake adabweraku Harare wina adampatsa nsalu ndiponso wina ankamubwereka
zovala pa maulendo ena monga popita kumowa.
9. “Iwe, sindiwe mwana wanga chifukwa undichititsa manyazi ndi kuba kwako.”

a. Mawuwa adabwera kwa Nthondo motani?

mmaloto
b. Nthondo anali kuti panthawiyi?
Ku Kapata
10. “Kuyendakwina………..Ha! kuyenda uku nako. Tiona nako malodza lero.”
a. Nthondo ndi anzake anali kuti panthawiyi?

b. Chidawadabwitsa nchiyani anthuwa?


c. Ndi zikhulupiliro zazipembedzo ziti zili pamenepa?
Chipembedzo cha makolo chomwe Nthondo ndi anzake amadziwa pomwe iwo

ankathira mfunde (nsembe) ndi kumaimbira pofuna mvula komanso chipembedzo


chenicheni chomwe adachiona patsikuli.
MUTU 5 : UKULU WAKE

 Nthondo atakula adasiya kuyendayenda ndi kuba.


 Adayamba kumakhala ku mabwalo kumagwira ntchhito ndi akuluakulu. Nthondo

adaphunzira izi:
i. Kusoka mphasa

ii. Kusema mipini

iii. Kumanga masindwi a nyumba


iv. Adaphunzira kuweruza milandu popeza atsibweni ake adali mfumu

 Sankakana akamtuma.
 Atsibweni ake adampatsa mkazi koma iye adamkana chifukwa anali wamng’ono.
 Wina adamulangiza kuti sibwino ukwatira msuweni wako popeza amanyada. Msuweni
wa Nthondo ndi Mdzitula.

 Nthondo adakayenda kumudzi wa Mnjondo komwe adakaoneka mbeta. Adauza


atsibweni akekuti akamfunsire mbeta.
 Maonekedwe a mkazi yemwe Nthondo adamuona : wamng’ono thupi, wamtali
komanso woyera.
 Mkazi wa Nthondo adakhwima. Amayi ake adapita kwa alongo a Mnjondo
(namkungwi)atatenga nkhuku yonenera.
 Apongozi ake a Nthondo adafulula mowa nakawuza akumudzi kwawo kwa Nthondo.
 Nthondo adapereka mphasa mahumi awiri kwa a Mnjondo ndipomwambo
wachinamwali unakonzedwa. Mphasa zina anasoka yekha koma zina anampatsa
abwenzi ake.
 Ntondo amatcha misampha nakola nkhwali, nkhanga ndi njiwa. Iyenso amachita

uzimba kotero anthu adakhumbira akadakhala mkamwini wawo.

 Atakhala kwa kanthawi Nthondo adapempha kuti amtenge chitengwa mkazi wakeyo
poti anali yekhayo mphwake wa mfumu. Makolo nawo adati adalibe mwamuna kotero

kuti Nthondo amawagwira pakati. Komabe adavomereza nawapempha kuti


akawasungire bwino mwana wawoyo.
 Mzungu adabwera kuderali ndi cholinga choti ayambitse sukulu.

 Mafumu adapemphedwa kuti avomereze kapena ayi.


 Atsibweni a Nthondo adauza mafumu monga a Mzinga, a Chikunje ndi aDzeya.
 Mawa lake mafumu pokambirana adakana sukulu poopa kuti mzinda utha
mongazidachitikira ku Mvera.
 Nthondo adapempha kuti iye ndi anyamata ena akuifuna poti adaona ubwino wake pa

Domwe pamene ankachita zamtengatenga.

 Mzungu adakondwera atamva kuti mafumu onse avomera zoti sukulu akuifuna. Iye
adapereka mabulangeti kwa mafumuwo ndi thumba lamchere.
 Adawapatsa kalata yoti akapereke kwa mzungu waku boma kuti adziwe.

 Atsibweni a Nthondo,a Dzeya, a Mzinga, a Chikunje pamodzi ndi Nthondo adapitaku


boma kukapereka kalata ija.

 Mzungu wa kuboma adawauza kuti akamange nyumba yabwino yophunziriramo.


Atafika kumudzi adauza anthu ndipo mfumu idapempha anthu kuti akolore mofulumira
kuti amange nyumbayo.

 Abambo ndi amayi adachita ntchito yanyerere namanga sukuluyo.


 Mzungu uja adabwera pa bulu wake kudzaona ngati sukuluyo idamangidwa koma
adapeza amfumu ali kumowa ndipo adayankhula ndiNthondo. Amfumu adakamwa
mowa kwa a Chikho; kunali kamowa ka azimu. Atachoka uko anakamwa mowa wa
zingwe womwe udawaledzeretsa kwambiri.
 Posakhalitsa mphunzitsi anabwera. Iye anavala zovala zoyera. Iye adawaphunzitsa

anthu kuwerenga ndiponso kupemphera.


 Mmodzi wa ophunzira pasukukukluyi adali Nthondo. Iye sadajombe ayi. Iye
adakondetsa kuwerenga ndikuyimba nyimbo zapamtima.

 Nthondo adamuyitana mphunzitsi uja kunyumba kwake kumene anamufotokozera


zamoyo wake. Iye adamufunsa chomwe angachite kuti akhalewabwino. Mzungu

adamuwuza kuti ayenera kuphunzira za mawu a Mulungu. Iye anavomereza mzungu


uja namubatiza.iye anakopa anthu ena ambiri.
MFUNDO ZAZIKULU (THEMES)

1. UMPHAWI
Nthondo ndi anzake adapita kumtengatenga ku Kapata chifukwa adalibe zovala
2. KUMVERA

Pamene adayamba kumakhala kubwalo ndi akuluakulu Nthondo anali omvera,


samakana akamutuma.
3. KULIMBA MTIMA
Pamene atsibweni ake ndi mafumu anakana zobweretsa sukulu m’mudzimo,
Nthondo sanachite mantha kutsutsana nawo akuluakuluwo, iye ananena
mwachimvekere kuti iye ndi ena achinyamata adaifuna sukuluyo

4. KUKHUMBIRA

Nthondo ndi anzake adakhumbira zomwe adaona pa sukulu yaDomwe kotero


mzungu atabwera ndi ganizo lofuna kutsekula sukulu m’mudzimo sanafune kuutaya
mwayiwu.

5. KHAMA
Nthondo sadajombe pamene anayamba sukulu ndipo iye adakondetsa kuwerenga

ndi kuyimba nyimbo za pamtima.


ZOYANKHULIDWA NDI ATENGAMBALI ENA
1. “Yanga ili kwa ayiya”

a. Amakonda kuyankhula mawuwandani?


Mkazi yemwe atsibweni aNthondo adamufunira kuti amukwatire.
b. Chifukwa chiyani Nthondo adakana kukwatira msungwanayu?
Adali wamng’ono popeza amakana kudya naye limodzi. Iye amati nsima yake ili kwa
amayi ake.
2. “Mkazi azikhala wotuwa ndiye mkazi wantchito, osakhala mkazi wosambasamba,

wadama, simkazi amenryo, sangathe kusunga mwamuna bwino”.


a. Perekani chitsanzo cha mkazi wodziwa kusunga mwamuna pa mutu umenewu.
Banja laMziza. Akazi awo si osalala koma amadziwa kuphika

b. Kodi chifukwa chiyani ena adalangiza Nthondo kuti sayenera kukwatira msuweni
wake?

amanyada
3. “Sindigathe kuchita choipa ngakhale wina atandituma sindingathe, koma ndi kulingilira
za mkazi kumene ndingampeze.”

a. Kodi Nthondo adampezamkazi pamudziuti?


Mnjondo
b. Kodi Nthondo adadziwa bwanji kuti pamudzipa padali mkazi?

Adamva anzake
c. Tchulani zoipa zomwe Nthondo ankachita poyamba.
 Kuba
 Ndewu
 Kugenda alendo odutsa
4. “Lekeni! Ndiye mkazia meneyu. Ichitha mbeta, ha! Siotukwanitsa. Ndikapita kumudzi
ndikauza atsibweni anga kuti akatume munthu wina akandifunsire mbeta.”

a. Lembani kusiyana kofunsa mbeta kale ndi makono.

Kale mnyamata amatuma wina kukafunsa mbeta mmalo mwake pamene masiku
ano munthu umafunsira wekha.
b. Kodi mawu oti “mbeta yotukwanitsa” atanthauzanji?

Mkazi okongola kwambiri kuposa mwini wake


5. “Tatiyeni pakomopa tikakambeko zobisa.”

a. Tchulani anthu awiri akuyankhulana pamenepa.


Nthondo ndi mlamu wake
b. Nchiyani akuti nzobisazi?

Kukafunsira mbeta pa mudzi waMnjondo


6. “Nthondo,ine sindifuna kuti ku mudzi kwa eni ukukhalaku uzikhala mwachibwana.
Kumva zotero ine toto. Atakuchotsa ku ukwati ine sindingalole kufunsira mbeta ina. Lero
wakula ndipo uzikhala mwachikulu ndipoudzaona anthu adzakulemekeza kuti
kwaNthondoku osati kungokhala mwamphwayi, sudzakhala ngati kamunthu koma
kagalu kachabe. Kumanga banja ndi ntchito.”

a. Adanena mawuwa ndani?


Mlamu wa Nthondo
b. Kodi mawuwa adanenedwa anthuwa ali kuti?

Iwo ali mnjira paulendo wopita kukafunsa mbeta


c. Kodi atafika kwa mbetayi adayankhulana ndiyani?

Mchimwene wake wamkaziyo


d. Tchulani maonekedwe atatu a mbetayi
 Wamng’ono thupi
 Wamtali
 Woyera
7. “Mom’muja ndidakuuziranimutu. Munthu azikhala wamnkhutu.”

a. Kodi mlamu wake wa Nthondo adamuuza chiyani?


Adamulangiza kuti ayenera kugwira ntchito molimbika ngati akufuna
kulemekezedwa. Iye adatinso ndi ntchito yomwe imamanga banja.
b. Kodi mawu oti “munthu azikhala wamnkhutu” atanthauzanji?
Munthu azimva kulangizidwa
c. Kodi mawuwa adanenedwa patsiku lanji?
Patsiku lomwemlamu wake adapita komutula Nthondo kubanja kwa Mnjondo.
8. “Amayi anga musamawathawe, ati ndinu mwana wawo.”

a. Tsimikizani kuti Nthondo adalandiridwa mokondwera kubanja? Perekani mfundo


imodzi.
Adapheredwa nkhuku ndi nsima yambiri
b. Kodi amayi ake a mkaziwa Nthondo adapereka chiyani kwa Nthondo kuti
asamaopane?

Mkanda
9. “Ha! Kodi! Wanena pafupi ndimtuma wina akanene kwa nkhoswe zakuchikazi”.
a. Kodi Nthondo akuyankhula ndi yani?

Atsibweni ake a Chembe


b. Nanga ndiuthenga uti oti wina akanene kwa nkhoswe zakuchikazi?
Uthenga wopempha chitengwa kuti Nthondo amutenge mkazi kupita naye kwawo
c. Chifukwa chiyani uthengawu sunakondweretse amake a mkazi wa Nthondo?
Iwo alibe mwamuna ndiye Nthondo ndi yemwe adawagwira pakati
10. Ha! Tambani mwaima a mfumu. Kodi ife sindife okalamba iyeyu ndi anzake amene

afuna. Mwana akalilira nyanga ya msatsi msemereni imfotere yekha.”


a. Adanena mawuwa ndani?
A Dzeya
b. Tchulani mafumu atatu omwe adali pamalowa.
A Dzeya, a Chikunje ndi a Mzingwa
c. Kodi mlembi amatanthauzanji ponena kuti “mwana akalilira nyanga ya msatsi
msemere kuti imfotere yekha”?
Alole sukuluyo ikhale m’mudzimo kuti Nthondo ndi anzake ailephere okha.
11. “Zija ninkanena zija nzimenezi. Nkwanji kuyankhulayankhula! Usakanene tsono izi
nzakuseri.”
a. Adanena mawuwa ndani?

Atsibweni ake a Nthondo.


b. Nchiyani chomwe woyankhulayi ankakana?
Sukulu
c. Chimachititsa kuti woyankhulayo anene mawu amenewa nchiyani?
Mphunzitsi adatumiza uthenga kwa a mfumu kuti auze anthu asagwire ntchito
komakuti apite kumapemphero zomwe zinali zachilendo kwa mfumuyi.
d. Mawuwa adanena kwa yani?

Nthondo
MUTU 6 : UFUMU WAKE

 Atsibweni ake a Nthondo aChembe adadwala ndipo anamwalira. Nthondo adatenga


mbuzi pokanena uthenga wamaliro kwa mfumu yaikulu.

 Anthu akulu pamudzipo adaitana akazi akukuluakulu nawafunsa uyo angathe kukhala
mfumu ndipo iwo adatchula Nthondo.

 Mfumu yaikulu inadziwitsidwa ndipo idabwera niveka Nthondo ufumu. Anamulowetsa

mnyumba nayamba kumulanga Nthondo malangizo osungiramudzi.


 Tsiku lina a Dzeya ndi a Mzingwa anabwera kudzaona Nthondo. Adafuna Nthondo

chifukwa chomwe iye salabada za mzinda ngakhale m’mudzimo mwakhala mukuchitika


maliro. Iye adakanitsitsa zamzinda nalamula kuti wofuna mzindaachoke m’mudzimo.
 Nthondo adadwala chibayo/chilaso ndipo adamwalira
 Anthu adamukumbukira Nthondo chifukwa chowabweretsera Chikhristu.

 Adakali ndi moyo ngati mfumu, Nthondo


i. Adathandiza a njala powapatsa zakudya
ii. Otetana adawaletsa ndi kuwakhalitsa mtendere.
MFUNDO ZIKULUZIKULU (THEMES)
1. IMFA
A Chembe ndi Nthondo adamwalira atakhala mafumu kudera kwawo.
Nthondoadamwalira atadwala chilaso.
2. CHIKONDI
Nthondo adaonetsa chikondi chake powapatsa chakudya anthu anjala
3. KULIMBAMTIMA
Nthondo sadazengereze koma kuonetsa kwa mafumu monga a Dzeya ndia Mzingwa
kuti ngati akufuna zamzinda achoke mdera lake.
4. KUSIYANA PAKATI PA ACHINYAMATA NDI AKULU
Achinyamata adakulupilira kuti sukulu ndiyofunika malinga ndi momwe adaonera pa
Domwe pamene achikulire samaifuna pofuna kupitiriza mzinda.
5. KUSIYANA PAKATI PA CHIKHRISTU NDI CHIKUNJA
Kusiyana kwaonetsedwa kudzera mwa Nthondo yemwe poyamba anali wakuba,
wadama komanso wandewu asanatembenuke kukhala Mkhristu ndi pano pamene
watembenuka. Iye akuthandizanso osowa chakudya powapatsa zakudya.
ZOYANKHULIDWA NDI ATENGAMBALI ENA
1. “Moni, Nthondo!”
“Moni !”
“Nkwabwinokodi?”

“Iyati nkoyipa.”`

a. Kodi Nthondo alik kuti panthawiyi?


Kwa mfumu yayikulu imene inagwira atsibweni ake ufumu
b. Chifukwa chiyani Nthondo akuti nkoyipa?

Atsibweni ake a mfumu Chembe amwalira


c. Kodi pokatula uthengawu, Nthondo adatenga chiyani?

Mbuzi
2. “A Mzingwa, tiyeni tichoke. Tamvani zachibwana akukamba mfumuzi”
a. Kodi adayankhula mawuwa ndani?

A mfumu Dzeya
b. Kodi a Mzingwa ndi yani?
Imodzi mwa mfumu zazing’ono
c. Kodi a Mzingwandi anzawo adali kuti panthawiyi?
Kunyumba kwa Nthondo
d. Kodi zachibwanazanji inkayankhula mfumuyi?

Nthondo adawuzamafumuwa kuti zamzinda zatha ndipokuti ngati akufuna


zamzinda achoke mdera lake.

MAFUNSO (ESSAY QUESTIONS)


1. Lembani zikhulupiliro zisanu zopezeka m’bukhuli.

2. Fotokozani maloto asanu omwe Nthondo adalota.


3. Umphawi ndi imodzi mwa mfundo zikuluzikulu m’bukhu laNthondo. Lembani
mfundo zisanu zotsimikiza mfundoyi.

4. Tsimikizani kuti Nthondo ndi olimba mtima polemba mfundo zisanu.


5. Tsimikizani kuti atengambali ena m’bukhuli ndi achifundo polemba mfundo
zisanu.

6. Tsimikizani polemba mfundo zisanu kuti milandu yambiri m’nkhaniyi


simaweruzidwa mwachilungamo.
7. Fotokozani anthu asanuomwe adamwalira m’bukhuli ndipo fotokozani

mmeneimfazi zikanatha kupewedwera.


TIYANKHE BWANJI MAFUNSO

Poyankha mafunso ali pamwambawa, ophunzira ayenera kutsata izi:

 Kulemba chiyambi chachifupi.

 Kulemba mfundo ili yonse m’ndime yake


 Mfundo zilembedwe mwachindunji komanso zizionetsa mfundo yeniyeni komanso

ziganizo zothandizira.

 Kulemba mfundo ziwiri mnime imodzi kumasokoneza ochonga ndipo mapeto ake
malikisi aaperekedwa a mfundo imodzi basi

 Ophunzira azitha kutchula mayina a atengambali osiyanasiyana komanso malo komwe


zomwe akulembazo zidachitikira.
SAMPLE QUESTION PAPER BY MANEB

Yankhani funso limodzi pa bukhuli m’ndime zofotokozedwa bwino.

1. Fotokozani kufunika kwa maloto anayi amene Nthondo analota pa unyamata wake.
Nthondo nanalota maloto osiyanasiyana omwe anali ofunika kwambiri pa moyo wake.
Mfundo yoyamba pamene adamangidwa chifukwa chakuba maungu atatu m’munda
mwa bwana wake nkuponyedwa mu gadi ku Harare Nthondo analota atalowa mdziko

labmdima. Mnyamata wina amene kale analasidwa ku munda uja adayamba


kumuthamangitsa, koma samaonetsetsa chifukwa cha mdima uja. Adangoona kuti mano
ake asanduka aatali. Nthondo adayesa kuthawa koma mnzakeyo sadamuleke. Nthondo

adadzidzimuka ndi mantha ambiri


Maloto amenewa anali ofunika popeza anali kumukumbutsa zoipa zomwe iye adachita
ku mphala kuja pamene adaphetsa mnzake yemwe anamukakamiza kuti amperekeze
kukaba miside. Uku kunali ngati kumchenjezanso kuti sayenera kubwereza zoipa.
Mfundo yachiwiri ikudzanso pamene tikuona Nthondo adalota akuthamagitsidwa ndi

mikango iwiri. Ali mndende ku Harare kuja pamene adamenya ndi kukomola mnzake,
iye adalota atapita ku uzimba ndi mnzake ndipo mikango iwiri imamuthamangitsa
nimugwira ndikumudya.
Atadzidzimuka Nthondo adayamba kulingalira kuti mwina panali wina amene

adamuchitira mankhwala kuti azichimwa popeza anzake amakhala mwamtendere.


Malotowa adali ofunika popeza adamuchenjeza Nthondo kuti zoipa zinali kubwera
mtsogol. Atachoka ku ndende iye adalingalira zopita kwawo. Mmbuyo mwake
kunapezeka kuti munthu yemwe Nthondo adammenya uja adamwalira kotero kuti
kupanda kuti iye adapita bwenzi atamangidwanso nkukaphedwa ku ndende.
Mfundo yachitatu ndi maloto a Nthondo pamene iye adalota munthu wina amene

adavala nsalu zoyera. Munthuyo adali ndi ndodo yowala ndipo adamuloza ndi ndodo

yakeyo ndi kuti: “Ndidzakulanga ukapanda kusiya zoipa zakozi”. Pamene adadzidzimuka
Nthondo adayamba kusisima chifukwa cha maloto amenewa.
Malotowa adali ofunika chifukwa adamuchititsa kutsutsika mumtima mwake ndipo
patsogolo pake ndi pamene adapanga chisankho chotembenuka mtima.
Mfundo yomaliza ikudza pamene Nthondo adalota ataona atate ake amene adafa kale.

Iye adalota atate akewo akupha nsomba ndipo Nthondo adapemphako koma iwo
adamukanira namuuza kuti si iyenso mwana wawo popeza akuwachititsa manyazi ndi
kuba kwakeko. Pamenepo Nthondo mosadziwika adabako nsomba imodzi. Atateto atate

akewo adayamba kumpitikitsa. Nthondo adayesetsa kuthawa ndi kuuluka koma


osatheka mpaka atate ake anamugwira pakhosi nabanika.
Malotowa adathandiza kwambiri Nthondo kusinkhasinkha zamoyo wake ndipo mapeto
ake adapanga chisankho chosiya kuba komanso makhalidwe onse oipa.

2. Tsimikizani popereka mfundo zinayi zosonyeza kuti Nthondo anali wamakhalidwe oipa

aadatembenuke mtima.

Nthondo adali munthu wabodza. Atsibweni ake a Nthondo atamufunsa za nkhunda


zomwe iye anaba, Nthondo anakana nauza atsibweni akewo kuti iye sanabe koma kuti
iye amangopita pafupi ndi chikundacho. Nthondo adati apa mwini wake anayamba
kufuula kutti iye wawabera. Koma patsiku lamlandu Nthondo sanatsutse zoti iye anaba.
Nthondo ananenanso bodza pouza amai ake kuti amasewera pamene anamufunsa
zakutuwa kwake. Choona chinali choti iye amamenyana ndi mnzake ku ubusa koma
sanafune kuti amakewo adziwe.
Khalidwe lina loipa la Nthondo ndi lakuba. Iye adayamba kuba ndiwo, mazira ndi zina
zamnyumba mwa amake pokumbira zimene anzake amadya kumphala. Ali ku mphala
Nthondo adaba zipwete kumunda kumene amasaka mbewa. Mwini zipwete anamuona
koma iye anathawira patchier osamugwiranso. Mmawa mwake Nthondo adaba nkhunda
ndipo eni ake adamuthamangitsa namugwira. Anthu adammenya Nthondo namuikira
nthenga zankhunda mtsitsi lake nayamba kuimba nyimbo uku akupita naye kwawo.
Atsibweni ake analipira mbuzi zisanu poombola Nthondoyo.
Nthondo akuonetsanso khalidwe lopanda chisoni komanso kuuma mtima. Ngakhale
adadziwa kuti nkhuku yomwe anzake adaba ndikupha idali ya amayi ake, Nthondo
sadaulule. Amake adadandaula kusowa kwa nkhuku yawo koma iye sadamve chisoni.
Iye adaumitsa mtima pofuna kusangalatsa anzakewo. Nthondo adagenda ndi mwala
alendo omwe amafunsa njira. Atanena kwa mfumu alensowo adalephera kuloza yemwe
adawagenda poti sanamudziwe. Amake a Nthondo adadandaulira nthndo kuti amange
nyumba yomwe idapsa ndi moto koma iye anangovomera koma sanamange. Nthondo
atauzidwa zakudwala kwa amake ndi munthu yemwe anatenga thumba la nyemba, iye
sanalabadire za matendawo.
Nthondo adali mwana wosamvera. Iye sadamveremayi ake atamupempha kuti
amumangire nyumba. Nthondo anakananso malangizo omwe munthu wina
amamulangiza. Ntondo anakalipira muntu yemwe adamulangiza kuti awamangire
amake nyumba pomuwuza kuti iye safuna kulangizidwa. Mayi ake atamuchenjeza
zakuyipa kwa kuba iye sanamvere. Anamkakamiza mnzake kukaba ndipo mnzakeyo
analasidwa nafa.

NHPL

You might also like