Treasa Cinyanja

You might also like

Download as docx, pdf, or txt
Download as docx, pdf, or txt
You are on page 1of 5

CINYANJA

2022 -2024
Grade 10,11, 12 & GCE
QUESTIONS
AND
MFUGULO
Nkhoma T.
ONANI ANGONI (K.D. Philip)

1 Kodi mfumu yankhanza ya Angoni inali yani?


2 Kodi ndani anatsogolera Angoni pocokera ku South Africa?
3 Pali nkhani zambiri zonena m’mene Angoni anawolokera zambezi. Fotokozani m’mene
Angoni anaolokera Zambezi kulingana ndi nkhani yogwiritsa nchito boti.
4 Pa mwambo wa cingoni ndani alowa ufumu?
5 Lembani zizindikiro ziwiri cabe za Angoni.
6 Buku la Onani Angoni ifotokoza za ulemu, kodi amaonetsa bwanji ulemu wao?
7 Kodi Angoni amathandizana bwanji?
8 Fotokozani zifikwa zomwe zinalengetsa kuti Angoni acoke kudziko la South Africa.
9 Fotokozani za maulendo a mafumu awa.
(i) Zwide
(ii) Zungendaba
(iii) Mputa
10 Kodi zakudya za a Ngoni zinali zotani? Chulani zitatu cabe..
11 Chulani kumene kupazeka mafumu acingoni awa masiku ano atacoka ku South Africa.
(i) Zwide
(ii) Mpezeni mwana wa Zungedawa
12 Perekani matanthauzo a maina awa:
(i) Mlaga
(ii) Limana
(iii) Ndani dzina la mkulu wa limana la Mpezeni?
13 Kodi kuthira nsembe ndikokutani? Chulani zifukwa zotsirira nsembe.
14 Fotokozani mene Angoni amayendetsera maukwati ao.
15 Angoni amagwiritsa nchito zida zosiyana-siyana ku Nkhondo.
(i) lembani zida za Nkhondo ziwiri.
(ii) Kodi mpeni waung’no unali kugwira nchito yotani?
16 Nenani zifukwa ziwiri zimene Angoni anali kumenyera nkhondo.
17 Kodi ndi cifukwa ciani pa maliro Amfumu anali kupha anthu ambiri ndi ziweto?
18 Angoni ali ndi magule osiyanasiyana. Chulani magule atatu ya angoni.
19 Mtundu uliwonse ulindi zizolowezi zao. Nanga angoni anali ndi zizolowezi zotani?
Nenani ziwiri cabe.
20 Fotokozani m’mane angoni anali kuikira munthu wakufa. Nanga cifukwa ninji anali kuika
motero.
21 Mau akuti ‘kuutha’ ndi mau acingoni. Kodi mauwa atanthauzanji?
22 Chulani mulandu wa ung’ono ndi malipilo ake.
23 Mulandu ikulu-ikulu inali cigololo ndi ufiti. Fotokozani mene anali kuweruzira mirandu
ikulu-ikulu imeneyi.
24 Kapolo anali kuchulidwa maina osiyanasiyana, monga asutu, afo, adzakadzi, akamtunda
ana a nsinaziwawa ndiena otero.
(i) Cifukwa ciani analiku chedwa maina amenewa?
(ii) Kodi maina onsewa anali kutanthauza ciani?

25 Chulani miko atatu amu Africa kumene kupezeka angoni masiku ano.
26 Lembani mwacidule nkhani zimene zipezeka m’buku la onani angoni.
MFUGULO
ONANI ANGONI (K.D.Philip)

1 Chaka Zulu
2 Zungendawa
3 Angoni atafika pa Zambezi anapeza munthu woolotsa anthu ndi boti ndipo mfumu
anamupempha munthuyo kuti awawo lotse. Pamene onse anatha kuoloka, anamgwira
munthuyo woolotsa namupha kuopa kuti angadzawolotserenso adani.
4 Mwana wamfumu woyamba kubadwa makamaka wamwamuna.
5 – Kubvala zikumba
- Kudoola makutu
- Cilankhulo cao
- Zakudya zao
6 Angoni amaonetsa ulemu polandila ndi popereka, kuitana ndi kubvomera, ulemu wa

Malo. Ngati amfumu akhala pa mupando ena onse akhala pansi. Pakudya ayamba ndi
akulu.

7 pogwirira pamodzi nchito za kumudzi, ku munda ndi zapamaliro. Amapatsana zinthu


mwaulere.

8 Angoni anacoka ku south Africa cifukwa ca nkhondo ya chaka ndi kucepa kwa malo.

9 (i) Zwide analowera kumpoto kudutsa dziko la Swaziland (iswatine) ndi ku

khala ca ku mumawa kwa dziko la Mozambique.

(ii) Zungendawa analowera kumpoto nafika ku Mozambique. Atakhalakopa

pang’ono anamenyana ndi gulu la zwide, atagonja anapitirira ulendo kuwoloka


Zambezi mu 1835 kulowa mu dziko la Zambia. Anamenyana ndi anthu
osiyanasiyana ndipo onsewo anawagonjetsa. Anapitirira ndi ulendo wake
kulowa mu dziko la Malawi ku kasungu anamenyanso ndi mitundu yambiri
m’malawi ndipo anawoloka mtsinje wa Rukulu ku lowa m’ dziko la Tanzania.

(iii) Mputa anacoka pamodzi ndi gulu la Mzilikazi kulowera kumpoto panjira ku

Transvaal anakangana ndipo gulu la mputa linapitirira ndi ulendo wao kuoloka
Zambezi ku mbali ya Tete ku lowa mu Mozambique. Anapitirira ndi ulendo
wawao kufika mu dziko la Malawi ku Domwe pafpi ndi boma la Dedza. Atamva
za mbiri ya angoni a zungendawa wochedwanso Magwambani anacoka pa
Domwe nalowa mdziko la Malawi ku mwera kwa Dedza ku Ncheu. Atasautsa ndi
nkhondo yake anaoloka m’tsinje washire ku fika ku Tanzania ku malo ochedwa
Mngongomwa (matengo). Anakomana ndi gulu la Zulu Gama a gulu la
Zungendawa. Anamenyana ndipo Mputa anapambana nakhala mfumu. Atakhala
mfumu kwa nthaw yaitali, Angoni a Zulugama anaukira gulu la mputa, mputa
anaphedwa ndipo pamene pa mene panathera gulu la mputa.

10 Nyama, mkaka, mapira ndi Mawere


11 (i) Gulu la Zwide ku Mozambique mdera la Shangaan

(ii) mpezeni ali ku Chipata mudziko la Zambia.

12 (i) Mlaga ndi kamudzi kakang’ono kopatuka m’mudzi wa ukulu.

(ii) limana ndi mabanja a gulu limodzi olimilana ndi kuthandizana.

(iii) Fundanimphasa

13 kuthira nsembe ndiko kuononga cinthu cina ca moyo kapena copanda moyo cifukwa

ca kupempha kanthu kwa mulungu.

Zifukwa za kutsirira nsembe:

-
Anali kuthira nsembe ngati m’banja mwaoneka zobvuta monga maliro, nthenda
ndi matsoka.
- Ngati m’modzi wa banja alota aliula nkhula ndi umodzi wa banja amene anafa
kale.
- Munthu anafa kale ali kupempha kanth kena.
14 Amaloola, kutenga Cuma ca ziweto kapena ndalama ndikupereka ku banja la makolo a
mkazi.

15 (i) - lihawo

- mkondo

- mbemba

- mpeni

(ii) Mpeni waung’ono unali wocotsera minga kapena cida pa thupi ngati umodzi
walasidwa ndi mdani.

16 - Cifukwa ca kumvera ndi kutsata malamulo amfumu yao.

- Kuti apeze njira yopitirira paulendo wao.

- apeze zakudya za paulendo.

- kukulitsa gulu lao ndi kuculutsa Cuma cao

17 Anali kupha anthu ambiri ndi ziweto kuti akhale msamiro ndinso kuti anthu adye pa
maliro.

18 Ligubo, ngoma ndi citoto mkwenda

19 - kumanga mdzi yao yaikulu ndipo moyandikana.

- kugula nsalu zikulu-zikulu

- kudya nyama ndi kusunga zida

- samaopa kupha munthu cifukwa ca kuzolowera nkhondo.

- kuphunzitsa ana amuna ndodo kuti akhale ocenjera ndi olimba mtima pa
kumenyana.

20 Anali kupinda maondo amunthu wakufayo ndi kummangirira mcikopa kapena nsalu
atammanga conco anali kumkhazika cansonga pamodzi ndi zida zake.

Anali kucita tero cifukwa anali kukhulupirira kuti msirikari wa nkhondo sagona.

21 Mau akuti ‘kuutha’ atanthauza kukonza pena kumanga kwake kwa maliro.

22 kulankhula mau oipa, kuonga zinthu za eni dala pena mwa ngozi

23 wogwidwa cigololo anali kuphedwa. Wogwidwa ufiti nayenso anali kupedwa ndi

mkondo. Ena anali kuperekedwa kwa mpondera(womwetsa mwavi)

24 (i) cifukwa kapolo wacita cinthu coipa kwa mbuyake.

(ii) kutanthauza kuti ndi anthu ogwidwa.

25 Zambia, Zimbabwe, Malawi,Mozambique, Tanzania

26 Mbukuli Manalembedwa za Maulendo, Ufumu ndi Ulamuliro ndinponso Nsembe,

Miyambo ndi Magule

You might also like