Download as pdf or txt
Download as pdf or txt
You are on page 1of 16

NKHANI YOMVETSA CHISONI

YA DZIKO LA MALAWI

Kalata ya Aepiskopi Akatolika ku Malawi

Lamulungu Lachiwiri M’nyengo ya Lenti,


25 February, 2024

Zikomo Abale ndi Alongo mwa Khristu,


Tikukulonjerani m’dzina la Yesu Khristu amene ali Ambuye ndi
Mpulumutsi wathu. M’nyengo ino ya Lenti, tikupemphedwa kuti
tisinkhesinkhe za moyo wathu mowunikiridwa ndi Mthenga wa
Yesu Khristu womwe ukupezeka m’Baibulo ndiponso potsata
chitsanzo cha Ambuye chimene adatiwonetsa pamene adali
pakati pathu zaka mazana awiri zapitazo. Pa Tsiku la Phulusa,
tidapakidwa phulusa pamphumi mau awa akunenedwa kuti:
‘Lapani ndi kukhulupirira Mthenga Wabwino’. Mau amenewa
amatitsogolera m’nyengo ya Lenti pamene timakumbukiranso
misteri za Masautso, Imfa ndi Kuuka kwa Ambuye Yesu.
Nthawi ino ya Lenti, tikusinkhasinkanso modzifunsa kuti, kodi
ngati dziko la Malawi, tili pati? Chaka chino tikwanitsa zaka
zinai tili mu ulamuliro wa Boma la ‘Tonse Alliance’. Ngati
Amalawi atadzifunsa kuti, KODI MOYO WATHU WASINTHA
POYEREKEZA NDI M’MENE UDALIRI ZAKA ZINAI ZAPITAZO?’
Yankho la Amalawi ambiri ndi lakuti, PALIBE CHIMENE
CHASINTHA M’MOYO WATHU. Ndi zowonekeratu poyera kuti
zimene Boma la Tonse Alliance linkalonjeza, palibe chimene
chikukwaniritsidwa.
1
1
Ndi zoona kuti dziko la Malawi lakhala likukumana ndi mavuto
osiyanasiyana monga mliri wa COVID-19, mavuto a ngozi zodza
mwadzidzidzi ngati Namondwe wa Freddy, chilala, kusefukira
kwa madzi ndi zina zotero. Mavuto amenewa asokoneza
ndondomeko zogwirira ntchito, anthu ambiri adataya miyoyo
yawo, midzi yochuluka idakokoloka ndi madzi ndi kuwononga
katundu wambiri wa anthu. Komabe, pa nthawi yomweyi,
takhala tikuwona kulephera kwa atsogoleri athu pa zinthu
zosiyanasiyana. Atsogoleriwa, amangobwebweta kapena titi
kulubwalubwa ndi kumanena zinthu zopanda pake mosafuna
kusunga zomwe adalonjeza kwa anthu a dziko lino. Ndipo
m’malo moti azikwaniritsa malonjezo akale, pano ayambanso
kulonjeza zina zatsopano zimene sizingakwaniritsidwe
mpang’ono pomwe. Kodi nkhani ingokhala yomangolankhula
mau opanda pake? Mau opanda pake tikunenawa akhala
akulankhulidwa pa mitu yotsatirayi:

1. Mikumano yopanda phindu ndi a President


Amalawi anzathu, pokwaniritsa udindo wathu wolankhulira
anthu ovutika, ife takhala tikuyesetsa kukumana ndi a President
maso ndi maso maulendo angapo koma sitikuwona kusintha
kulikonse pa kayendetsedwe ka Boma ndiponso pa chisamaliro
cha anthu osauka. Takhala tikuchenjeza atsogoleri oyendetsa
Boma kuti ngati kusayendetsa bwino kwa boma kupitirira,
zinthu zidzanka ziyipirayipira m’dziko lino kuposa m’mene
zidalili zaka zinai zapitazo. Mwatsoka ilo lomwe, zomwe
tidanenazi, zikupherezera. Pamene kukumana kwathu ndi a
President kwakhala kopanda phindu, ife ngati Akhristu tili ndi
chiyembekezo chakuti tsiku lina zinthu zidzasintha. Pofuna kuti
2
kusintha kumeneku kuchitike mwamsanga, tafuna kuti kulira
kwa Amalawi ambiri osauka ndi ovutika kumveke ndipo
pakuyenera kukhala njira zina zakuti kusinthaku kutheke.

2. Katangale
Pakali pano, katangale wafika poyipa m’dziko lino. Kuyambira
akuluakulu mpaka kutsika m’munsi, anthu odziwika
akusanduka olemera kosasimbika pakanthawi kochepa
podyera anthu osauka ambirimbiri masuku pa mutu.
Chokhumudwitsa ndi chakuti katangale walowerera m’magawo
osiyanasiyana a moyo m’Malawi muno. Umu ndi m’mene zinthu
ziliri masiku ano. Anthu ochita katangale akhala akuyesetsa
kuchita zinthu zofooketsa ndi kulepheretsa mabungwe
olimbana ndi katangale kuti asagwire ntchito yawo mokomera
Amalawi komanso chilungamo. Zimene zikuchitika tsopano ndi
kungobwatikidwa kapena titi kupusitsidwa kuti tiziti ntchito
yolimbana ndi katangale ikuchitika. Ngati anthu okhulupirira
Yesu Khristu, tikuyenera kukhalabe ndi chiyembekezo, osataya
mtima. Potsamira pa Chiyembekezo Chachikhristu, ife
tikuyamikira amene amadzipereka modzikhuthula, ndipo
chitsanzo ndi Bungwe la Zamalamulo (Malawi Law Society) ndi
ena otero, amene amakhulupirira kuti katangale ndi tchimo
ndipo akuchita ntchito yotamandika kulimbana ndi mchitidwe
woyipawu. Iwowa sanatayebe chiyembekezo chakuti,
chilungamo ndi chotheka kuchikwaniritsa pansi pa utsogoleri
wabwino.

3
3. Pansi pa Ulamuliro wa Boma la Tonse Alliance
Kodi chikuchitika nchiyani ndi atsogoleri athu? Ife tazindikira
kuti zina zokhumudwitsa zimene zikuchikita atsogoleri athu
akuona ndiponso nthawi zina akukhudzidwa ndi zotsatirazi:
a. Nkhani ya kuchepetsa ndalama zogwiritsa ntchito
atsogoleri, ndi nkhambakamwa chabe. Nkhani ndi yakuti,
palibe chimene chasintha. Amangopereka zifukwa zopanda
pake kuti akhale paulendo womwe umasowa ndalama
zambiri zapathumba (allowances) komanso anthu
ochuluka okhala nawo pa maulendowa. Mchitidwe
woterewu wasanduka ngati chizolowezi chomwe
chimawonongetsa ndalama zambirimbiri zomwe ndi
misonkho ya anthu osauka.
b. Anthu akudabwa kuti zikutheka bwanji kuti anthu amene
akufufuzidwa pa nkhani ya katangale, akupatsidwa mwai
wochita malonda osowa ndalama mamiliyoni a madola
pamene dziko lathu likusowa ndalama zakunja.
c. Madilu okayikitsa pakati pa Boma ndi ogulitsa katundu
angosanduka chizolowezi pakati pathu. Palibe kuganizira
anthu osauka amene amazunzika tsiku ndi tsiku kuti apeze
zosowa zawo za tsiku ndi tsiku. Kulira kwa anthu osauka
sikumveka chifukwa cha ndondomeko zolakwika zogulira
katundu m’maunduna ndi m’mabungwe ena aboma. Izi
zimachitika chifukwa cha anthu amene amadzitcha
amkhalapakati omwe ena mwa iwo ali ndi ubale ndi alangizi
a President ku Nyumba ya Boma.
d. Tawona akuluakulu ena okayikitsa akutetezedwa popanda
china chilichonse chomwe akuthandizapo pa ubwino wa
4
dziko lino. Izi zimachititsa kuti dziko lathu likhale pa
chiwopsezo chokhala ndi ngongole yambiri kuwonjezera
pa imene tili nayo kale.
e. Tawonapo mtolankhani wina amene akukhala mobisala
chifukwa chonena zoona zokhudza katundu wopita ku
gulu la Asilikari Ankhondo amene munthu wina
woganiziridwa kuti akukhudzidwa nkhani ya katangale
akuyenera kuperekera. Kodi iyi ndi njira yofuna
kutibwezeretsa ku ulamuliro wa chipani chimodzi?
f. Ndife okhumudwa kumva kuti pali mphekesera yakuti
anthu ena akufuna kusintha lamulo la chisankho lakuti
wopambana azipeza mavoti opesera theka la anthu ovota
(50% + 1). Kulimbikitsa maganizo otere, nkulakwa kwambiri
chifukwa kudzakhala ngati kufuna kusintha malamulo
oyendetsera dziko ngati momwe ena m’mbuyomu
ankafuna kuti mtsogoleri wadziko azitha kusankhidwanso
kachitatu. Ngati ndi zoona kuti anthu ena ali ndi maganizo
oterewa, ife tikuwalangiza kuti chinthu chanzeru
nkulekeratu kukhala ndi maganizo oterewa chifukwa
zidzakhumudwitsa anthu ambiri.
g. Mchitidwe wokonderana ndi vuto linanso pakati pathu.
Kalembedwe ntchito ka anthu m’boma kamawoneka kuti
ndi kokondera mtundu kapena chigawo chimodzi. Amalawi
onse ngofanana. Panthawi ya kampeni, tinkamva kuti
mchitidwe wokonderana udzakhala mbiri yakale. Koma
zimene tikuwona tsopano, zikusiyana ndi zimene
zinkalonjezedwa.

5
h. Pali mpungwepungwe wokhudza lipoti lonena za ‘Kusintha
ndi Kukonza Kagwiridwe ka Ntchito M’boma’ (Public
Service Reform Report). Anthu ambiri akuganiza kuti
mulipoti limeneli, muli Mfundo zabwino zambiri zothandiza
kukonzanso kagwiridwe ka ntchito m’boma koma
ndizodabwitsa kuti lipotili likusungidwa mwachinsinsi!
i. Kukuwoneka kuti a Tonse Alliance sakulabadira za
malonjezo amene adachita kwa anthu.
j. Pologalamu yopereka zipangizo zaulimi zotsika mtengo
yangosanduka ngati nthano chifukwa opindula ndi anthu
ochepa. Kodi feteleza uja Amalawi adawuzidwa kuti
adzagula pa mtengo wa K4,995 pa thumba limodzi ali kuti?
Zotsatira za izi, ndizakuti, dziko la Malawi likulephera
kukhala ndi chakudya chokwanira.
k. Mphamvu ya ndalama ya Kwacha yatsika kwambiri
pamene ndalama zimene anthu amapeza ndi zochepa.
l. Mazunzo a anthu okhala kumidzi afika podetsa nkhawa.
Mabanja ena akungogona osadya kanthu chifukwa
sangathe kugula feteleza pa msika. Vutoli lakulanso
kwambiri chifukwa chosowa mvula yokwanira.
m. Makolo ndi alezi akulephera kulipirira ana awo sukulu fizi
ndipo pachifukwa ichi, ophunzira ambiri sakupitiriza
maphunziro. Izi zidzalepheretsa dziko lathu kupita
patsogolo.
n. Miseu yathu ikunka iwonongekerawonongekera. Mwachi-
tsanzo, miseu yaikulu ya M1 ndi M5 ndi yochititsa manyazi
kuyendamo.

6
4. Mabwalo Amilandu
Ngakhale kumabwalo a Milandu, oweruza milandu adaleka
kugwira ntchito mwachilungamo ndipo m’malo mwake,
adalowerera mchitidwe wa katangale ndi wokondera. Kugula
oweruza milandu sichinthunso chotengedwa ngati
choletsedwa. Sichisinsinso ayi kuti anthu ena oyimila anzao pa
milandu (lawyers) akulemera popereka ziphuphu kwa oweruza
milandu pofuna kuti pasakhale chilungamo. Oweruza milandu
ena sawopa munthu wina aliyense chifukwa amadziwa kuti
palibe amene angawadzudzule. Amatenga zaka zambiri kuti
mlandu uthe, koma ngakhale amachita izi poyerayera, palibe
uyo amawadzudzula ndi kuwapatsa Chilango. M’malo mwake,
ndi anthu oterewa amene amakwezedwa pa udindo.
Tikukhulupirira kuti Unduna Wachilungamo ukubwezera
m’mbuyo chidwi cha a Bungwe la Malamulo (Malawi Law
Society) pa ntchito yawo yofuna kukhazikitsa lamulo lothandiza
kuti oweruza milandu azigwira ntchito yawo mwachilungamo.
Lamulo limeneli, ife tikugwirazana nalo chifukwa kukhala ndi
malamulo abwino, ndiye maziko a dziko lirilonse lofuna
kuthetsa katangale.

5. Kuzunza Anthu Achikulire Powaganizira kuti ndi Mfiti


Anthu ena achikulire ku Malawi kuno, akukhala ndi mantha
chifukwa chakuti moyo wawo uli pachiwopsezo. Anthu ambiri
achikulire, amuna ndi akazi, ali pachiwopsezo choganiziridwa
kuti ndi mfiti ndipo amachitiridwa nkhanza za mitundu
yosiyanasiyana komwe nkuphwanya ufulu wawo wachiba-
dwidwe. M’chaka cha 2023 chokha, achikulire okwana 78
adzazunzidwa ndipo 25 mwa amenewa, adaphedwa pa zifukwa
7
zoganiziridwa kuti ndi mfiti. Nkhani yomwe idachitika posa-
chedwapa (pa 27 December 2023) yokhudza kuzunzidwa kwa
mai wina dzina lake Khristina Chiwoko, wa zaka 66 ndipo
amachokera m’mudzi wa Mwanza, Mfumu yaikulu Chiwere
m’boma la Dowa, ndi chitsanzo cha nkhanza zochitira anthu
achikulire m’Malawi muno. Mai Khristina adafotseredwa mpaka
m’khosi kwinaku akufunsidwa ngati amachitadi zaumfiti.
Pamene nkhani zozunza amai ndi abambo achikulire zikunka
zichulukirachulukira, tawona kuti palibe chimene Boma
likuchitapo mogwira mtima pofuna kuthetsa mchitidwewu.
Njira imodzi yolimbikitsira chitetezo ndi chilungamo cha anthu
achikulire, ndiye kukhazikitsa malamulo okhwima otetezera
anthu oterewa. Boma silikusonyeza chidwi chenicheni chofuna
kubweretsa ndi kukambirana Bilu Yokhudza Anthu Achikulire
ku Nyumba ya Malamulo kuti likhale lamulo. Lamuloli
litakhazikitsidwa, pali chiyembekezo chakuti amuna ndi akazi
achikulire adzatetezedwa ndipo adzakhala ndi mwai wopeza
chilungamo pa nkhani zowakhudza.

6. Kulemekeza ndi Kusamalira Chilengedwe


Ndi chachidziwikire kuti dziko lapansi liri pa chiwopsezo
chachikulu chifukwa chakusintha kwa nyengo ndiponso
chifukwa cha kulephera kwathu pa ntchito yosamalira za
chilengedwe. Ngati tipitiriza monga tikuchitiramu, mibadwo ya
mtsogolo sidzakhala ndi podalira pa moyo wao. Dziko la Malawi
likuyenera kulemekeza mapangano amene lidachita
mokhudzana ndi kusintha kwa nyengo ndi chilengedwe.
Tikupempha Boma kuti liyikepo chidwi pa mitu yotsatirayi:

8
a. kusamalira ndi kusunga bwino nkhalango zathu;
b. kupitiriza ntchito yobzala mitengo;
c. kupeza njira zina zophikira m’malo mwa Makala;
d. kulimbikitsa kugwiritsa ntchito mphamvu ya dzuwa ndi
njira zina zophikira;
e. kulimbikitsa njira zina zokhazikika pogwiritsa ntchito
zachilengedwe;
f. kupititsa patsogolo njira zamakono zaulimi, mwachitsanzo,
njira za mtayakhasu, ndi zina Zotero.

7. Kufika Pothera Moyo (Bagamoyo) M’malo Mofika ku


Dziko Lachilonjezo
Amalawi anzathu, tili ndi chisoni chachikulu ponena kuti,
chifukwa cha mavuto ochuluka amene atchulidwa pamwa-
mbapa, Amalawi ambiri ataya chiyembekezo ndi Boma la Tonse
Alliance ndi utsogoleri wake. Ngakhale kuti tidali ndi
chimwemwe ndi chiyembekezo, kuti Boma la Tonse Alliance
lidzatitsogolera bwino pa ulendo wopita ku dziko lachilonjezo,
koma patangopita zaka zinai zokha, Amalawi ambiri
takhumudwa kupatula anthu ochepa okha amene zao
zikuwayendera chifukwa ali paubale ndi akuluakulu ena. Pakali
pano, Malawi wafika ku Bagamoyo – womwe ndi mzinda ku
gombe la Nyanja yamchere m’dziko la Tanzania. Kumeneku,
akapolo ogulitsidwa ankati akafikako, ankatayiratu mtima ndi
chiyembekezo chokhalanso mfulu.
Ifenso ngati Amalawi, m’malo mofika ku dziko lachilonjezo ndi
laulemelero, tikuwumirizidwa kukhalabe m’dziko limene
tinkafuna kulisiya, lomwe ndi dziko la njala, matenda, umphawi,
katangale ndi zina zotero. Motero, Amalawi ambiri akuona kuti,
9
palibe chimene chingachitike kuti dziko lino lisinthe kapena kuti
moyo wa anthu upite patsogolo kupatula anthu ochepa okha
amene zao zikuwayendera bwino. Sakuwona wina aliyense wa
m’boma amene amakhudzidwa ndi mavuto awo kapena amene
angathe kusintha zinthu mowakomera. Akudzifunsa kuti kodi
atsogoleri a Boma limeneli angakayankhe zotani kwa Mulungu
pa funso lomwe Chautayo adafunsa Kaini loti, ‘Kodi mbale wako
Abele ali kuti?’ Mwinatu atha kuyankha monga adachitira Kaini,
kuti: “Sindikudziwa. Kodi ndine mlonda wa mbale wanga?”
(Gen. 4:9).
8. Mikangano ya M’zipani Zandale
Ndife okhumudwa kuwona kuti mikangano ya m’zipani zandale
ikupitilira. Mikangano yosathayi, mathero ake akukhala
kuchotsana m’zipani kapena kutenga ziletso ku mabwalo
amilandu. Mkuwona kwathu, zimene zikuchitikazi zikubwezera
m’mbuyo ufulu wa demokalase ndipo zili ndi kuthekera
kowononga dziko lathu ndi kukulitsa umphawi wadzawoneni.
Kodi anthu amene akukanganawa, akuchita izi pofuna
kudzatumikira pa za ubwino wa Amalawi kapena akungofuna
kudzakwaniritsa zolinga ndi zofuna zawo? Amalawi akulakalaka
patakhala zipani zodzagwira ntchito zokomera nzika zonse
m’dziko m’malo mongokwaniritsa zofuna zawo zokha.

9. Kuyipa kwa Kusalolerana pa Zipembedzo


Pakatipa, tawona kuti, kusalolerana kwa anthu a zipembedzo
zosiyanasiyana kukunka kulirakulira ndipo pakhala pakuchitika
nkhanza zovulazana komanso zonyozana m’madera ena a dziko
lathu lokonda mtendereli. Ife tikudzudzula mwamphamvu
10
mchitidwe wina uliwonse wochitirana nkhanza zamtunduwu.
Mchitidwe wa nkhanza ngosayanera kuchitika masiku ano a
demokalase makamaka m’dziko ngati lino lomwe ndi lowopa
Mulungu, lachikondi ndi lolemekeza malamulo ndiponso
lokhala ndi ufulu wachipembedzo.
Tikupempha nzika zonse kuti zilemekeze zikhulupiriro za anthu
ena ndi kulola kuti anthu enawo azipembedza mwaufulu.
Tikupemphanso magulu achitetezo kuti akawona zoterezi
zikuchitika, azithamangirako msanga ndiponso mosakondera.
Tikupempha atsogoleri onse azipembedzo, Akhristu kaya
atsogoleri a Zipembepedzo zina, kuti tizilimbikitsa chikondi,
mtendere, umodzi ndi chilungamo. Kuchita zinthu zotsutsana
ndi izi kumachokera kwa woipa uja, yemwe ndi Satana.

10. Kukonzekera Chisankho cha 2025


“Zoona, Ine ndiye amene ndimadziwa zimene ndidakukonzerani,
zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi
chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo”, atero Ambuye
(Yeremiya 29: 11). Pamene Mneneri Yeremiya ankanena mau awa,
nkuti Aisraele ali ku ukapolo chifukwa chosamvera Mulungu.
Mneneri wonama wina adawuza Aisraele kuti Mulungu
adzawapulumutsa ku ukapolo waku Babiloni pakapita zaka
ziwiri. Koma Mneneri Yeremiya adabwera kudzakonza zinthu. Iye
adalengeza nkhani yokhumudwitsa yoti Aisraele adzakhala ali
mu ukapolo wa ku Babiloni kwa zaka 70. Izi sizimene Aisraele
ankayembekezera kumva chifukwa zinkatanthauza kuti, mbadwo
wathunthu udzafera ku ukapolo. Koma chimene Mulungu
akufuna kuti Aisraele adziwe ndi chakuti, Iye ali ndi dongosolo
lothandiza anthu a mfuko losokeralo. Iwo akuyenera kusungitsa
11
chikhulupiriro chao mwa Mulungu. Chiyembekezo chimenechi,
chidzawalimbitsa mtima m’zaka zambiri zakutsogolo.
Potengera zokhoma ndi mavuto amene afotokozedwa mkalata
yino, titha kuganiza kuti dziko lathu lino ndi lotembereredwa.
Komatu izi sizowona. Mulungu sataya ana ake. Ifenso, pamene
nthawi ikupita, tikuyenera kukhazikika pa chikhulupiriro
chanthu chakuti Mulungu sangatitaye kapena kutiyiwala.
Chikhulupiriro chathu mwa Mulungu wachifundo, chitithandize
kukhala ndi mphamvu m’zaka zikubwerazi tikusendera
pangónopangóno ku chitukuko ndi ulemelero.
Mulungu amafuna kuti tigwirizane naye pofuna kuti tichoke
m’masautso amene tili nawo. Njira imodzi yogwirizana naye,
ndiye yakutengapo gawo mwanzeru pa chisankho
chikubwerachi. Ngakhale kuti mavuto amene tikukumana nawo
ndi chifukwa cha kulephera kwa atsogoleri amene satha
kuyendetsa bwino dziko; ifenso ngati nzika komanso ngati
anthu amene timavota, mavutowa ali pakati pathuwa ndi
chifukwanso chakuti ifeyo tidalephera kusankha atsogoleri
oyenera. Motero, pamene tikuyandikira chisankho cha 2025,
tikufuna kukumbutsa aliyense kuti:
a. Kusakhala ndi chidwi ndi zandale kumatanthauza
kusalabadira za moyo wako, za ubwino wako, za ntchito,
ufulu ndi tsogolo lako.
b. Ndale zimasowa maziko amphamvu, zovomerezeka, ndi
zotsata mfundo za umunthu ndi zothandiza.
c. Nkofunika kuti aliyense akhale ndi ufulu wovota pofuna
kuti amene angasankhidwe akhale ovomerezeka ndi
anthu.

12
d. Ndi chinthu choyenera kuti achinyamata agwiritse
ntchito ufulu wao wovota Chifukwa zotsatira za
chisankho ndi zimene zidzawongolere tsogolo lawo.
e. Nzika iliyonse ili ndi udindo wolankhula za ufulu ndi
chilungamo.
f. Pamene tikuyandikira chisankho, m’Malawi aliyense
akuyembekezeka kukhala nzika yabwino popewa
nkhanza ndi makhalidwe owononga zinthu.
g. Mabungwe ofalitsa mau, ndalama, mphamvu ndi boma
kapena zipani, zingathe kugwiritsidwa ntchito molakwika
ndi anthu andale ndi Cholinga chofuna kupeza mavoti
ochuluka.
h. Ndikofunikira kufunsa oyima nawo pa chisankho
chikubwerachi kuti mbiri yao pankhani yotumikira anthu
ndi yotani. Tisasankhe munthu pa chifukwa chimene iye
ali kapena komwe akuchokera kapenanso potengera
maubale ake ndi anthu ena.

11. Kuwombamkota
Sitikuyenera kupitirira monga m’mene zinthu ziliri m’dziko lathu
lino. Atsogoleri athu asiye mkhalidwe wophangira ndi wotumikira
okhawo amene adawasankha. Tikusowa kupatsa mphamvu
mabungwe amene amayenera kuyang’anira zochita za Boma
mopanda andale kulowererapo. Aphungu aku Nyumba ya
Malamulo, akuyenera kusiya mchitidwe womangokamba
zandale. Zomwe tawona posachedwapa ku Nyumba ya
Malamulo, ndi zochititsa manyazi. Tikuwona ulamuliro wopanda
masomphenya m’dziko muno. Ili ndi gwero la mavuto amene
tikukumana nawo. Pokhapokhapo atsogoleri atasiya mkhalidwe
13
wadyera ndi wophangira, nakhala ndi chidwi choyendetsa bwino
dziko lino ndi kuyesetsa kuthetsa katangale, zinthu zitha
kusintha. Koma tikapanda kutero, tidzapitilira kukhala m’mavuto
amene tili nawo tsopano. Tikupempha kuti pakhazikitsidwe
lamulo lomveka bwino limene lidzathandize kuwongolera bwino
ntchito za ku Mabwalo Amilandu. M’dzina la Ambuye Mulungu,
tikupempha atsogoleri athu kuti amve kulira kwa anthu osauka
ndi kuchitapo kanthu.
Tipempherenso kuti nyengo ya Lent ino ikhale yotithandiza
kutembenuka mtima ndipo chikondwerero chathu cha Kuuka kwa
Yesu Khristu pa chaka cha Paska chikhale chiyambi cha moyo
watsopano wa Amalawi onse. Tipemphe kuti Yosefe Woyera,
bambo womulera wa Ambuye Yesu Khristu, ayang’anire dziko lathu
kuti Mulungu aike mwa ife mtima wodzilemekeza, wachilungamo,
wokonda dziko lathu, wachikondi ndi wamtendere.
Tikupereka zosinkhasinkha zathuzi mowunikiridwa ndi Mzimu
Woyera ndiponso mu uneneri wa Maria, Mfumukazi ya Malawi
ndi Africa.

Mlungu dalitsani Malawi,


Mumsunge m'mtendere.
Gonjetsani adani onse,
Njala, nthenda, nsanje.
Lunzitsani mitima yathu,
Kuti tisaope.
Mdalitse Mtsogoleri nafe,
Ndi Mayi Malawi.

14
Malawi ndziko lokongola,
La chonde ndi ufulu,
Nyanja ndi mphepo ya m'mapiri,
Ndithudi tadala.
Zigwa, mapiri, nthaka, dzinthu,
N'mphatso zaulere.
Nkhalango, madambo abwino.
Ngwokoma Malaawi.

O Ufulu tigwirizane,
Kukweza Malawi.
Ndi chikondi, khama, kumvera,
Timutumikire.
Pa nkhondo nkana pa mtendere,
Cholinga n'chimodzi.
Mayi, bambo, tidzipereke,
Pokweza Malawi.

15
National Anthem in Chichewa
Signed:
Most Reverend George Tambala President, Archbishop of Lilongwe
Right Reverend Montfort Stima Vice President and Bishop of
Mangochi
Most Reverend Thomas Msusa Archbishop of Blantyre
Right Reverend Peter Musikuwa Bishop of Chikwawa
Right Reverend Martin Mtumbuka Bishop of Karonga
Right Reverend John Ryan Bishop of Mzuzu
Right Reverend Peter Chifukwa Bishop of Dedza
Right Reverend Alfred Chaima Bishop of Zomba
Right Reverend Yohane Nyirenda Auxiliary Bishop of Mzuzu
Right Reverend Vincent Mwakhwawa Auxiliary Bishop of Lilongwe

16

You might also like