Download as pdf or txt
Download as pdf or txt
You are on page 1of 11

MATAPWATA CLUSTER EXAMINATIONS BOARD

2022 JUNIOR CERTIFICATE MOCK EXAMINATIONS

CHICHEWA

Subject no: J022/11

Time Allowed: 1h 45 min

MONDAY, 30 May, 2022

PEPALA LACHIWIRI
(Malikisi 50)

Malangizo

1. Onetsetsani kuti pepala ili lili ndi masamba Chongani Muno

otsindikizidwa asanu ndi awiri. Funso zomwe musalembemo
mwayankha
2. Lembani nambala yanu pamwamba pa masamba onse. 1

2
3. Yankhani mafunso onse mu gawo A, B ndi C.
3

4
4. Onetsani funso lililonse lomwe mwayankha pochonga mu
kabokosi kali ku tsogoloko. 5

5. Perekani pepalali kwa oyang`anira mayeso nthawi

ikakwana.

©MATAPWATA CLUSTER MOCK EXAMS 2022

GAWO A (Malikisi 20)

KUMVETSA NKHANI

1. Werengani nkhani ili m’munsiyi mosamala ndipo muyankhe mafunso

otsatirawo

TSOKA LA SELINA

Kodi mtsikana uli ndi zaka zingati? Adafunsa mokwiya namwino

pachipatala cha Ndatopa pamene amayetsera kuthandiza Selina m’chipinda
chomweramo madzi amayi. ‘ndili ndi zaka khumi ndi mphambu zisanu
zakubadwa’ adayankha Selina motsitsa mawu chifukwa cha ululu waukulu
omwe udakuta thupi lake panthawiyo.

Wakupatsa pathupipa ndindani? Adafunsanso namwinoyo pofuna kumvetsa

bwino za nkhaniyi popeza madzi adali atachita katondo, Selina
panthawiyi adali pafupi kuba mphasa. Selina adafotokodzera namwinoyo
nkhani yomvetsa chisoni.

Mangulenje adali dalaivala wa minibasi yomwe imandidutsa tsiku

lililonse ndikamapita kusukulu. Tsiku lina adandifunsa chifukwa chomwe
chimandipangitsa kupha nyerere tsiku lililonse. Nditamuyankha, iye
adandilonjedza kuti andigulira mabuku, makope, chikwama komanso
ndizikwera minibasi yakeyo mwaulere popita kusukulu. Ndinakopeka zedi
chifukwa Mangulenje adalidi bank yoyendayenda. Ndinaziyankhulira
muntima kuti chaka chokolola chafika, anzanga andimva madzi. Komabe
ndinamva Mangulenje akunong`onedzera kondakitale wake kuti ‘ndapeza
ndiwo’. Panthawiyi sindinathe kuganiza modzama chomwe amatanthauza
chifukwa cha chimwemwe chodzadza saya chomwe chinandiiwalitsa zonse.
Ndimangoganiza kuti akandigulira mabuku, masamu andidziwa kuti ndine
Selina Ngozo.

Mangulenje adakwaniritsa zomwe adandilonjedza choncho ubwenzi wathu

udafika pampondachimera. Adayamba kundinamiza kuti kugonana naye
kamodzi kokha sindingatenge mimba. Amabwereza kukamba mawuwa tsiku
lililonse tikakumana. Ndidakopeka mpaka kugona naye osaziteteza.
NAME __________________________________________ SCHOOL _______________________
Zinthu sizinayende monga momwe ndimaganidzira. Kamodzi komweko
ndidangodzindikira kuti ndine oyembekedzera. Ndidasweka mtima
poganidzira momwe makolo ndi anzanga angailandilire nkhaniyi.
Ndidaganiza zoyamba kudziwitsa Mangulenje nkhaniyi kuti tithandizane
maganizo.

Ine ndikuzidabwa kwambiri ndipo ndili ndi chikhulupiliro kuti ndili

ndi pakati. Ndidatero kufotokodzera Mangulenje nkhaniyi. Mphindi imodzi
idadutsa asanayankhe kanthu. Malovu otentha adadzadza mkamwa mwake,
Kusowa choyankha. Izi zinandidodometsa kwambiri. ‘Ndiye uchita
chiyani’? Adandifunsa ngati nkhaniyi sikumukhuza. Apa tidakangana
mwakanthawi, potsiriza Mangulenje adangoti zimenezo uziona wekha ine
ndapita. Ulendo udali omwewo. Apa ndi pomwe ndidadzindikira kuti
Mangulenje wandigwiritsa chikho mkati.

Nthawi yoereka idakwana, zoyankhulana za Selina ndi namwinoyo zidaleka

nthawi imodzi. Selina adavutika kubereka popeza ziwalo zake zidali
zisanakhwime. Pachifukwa ichi iye adabereka mwana wake panjira ya
opereshoni. Koma tsoka likalimba zinthu zimangoyenda modzondoka. Selina
adamwalira chifukwa chotaya magazi ambiri n’kusiya mwana wamng`ono
yemwenso adalibe mphamvu ndipo adamwaliranso patadutsa maora anayi.

Makolo ake polira ankangoti Se-Se-Se-lina msinje watinkanena udathera

mu siizi.

Tsopano yankhani mafunso otsatirawa:

a. Kodi Selina adali mwana wa yani?

________________________________________________________________
(malikisi 1)
b. N’chifukwa chiyani namwino adakwiya pamene amayankhulana ndi
Selina?
____________________________________________________________
__________________________________________________________
(Malikisi 2)
c. Perekani matanthauzo a mikuluwiko yotsatirayi:

3
NAME __________________________________________ SCHOOL _______________________
i. Wandigwiritsa chikho mkati

________________________________________________________________

ii. Kuba mphasa

________________________________________________________________

iii. Chipinda chomweramo madzi amayi

________________________________________________________________
(malikisi 3)

d. Perekani umboni uwiri zotsindika kuti Selina amalangizidwa

ndi makolo ake koma iye samamvera.

________________________________________________________________
________________________________________________________________
(malikisi 2)

e. Tchulani njira ziwiri zofalitsira uthenga wa maliro.

________________________________________________________________
________________________________________________________________
(malikisi 2)
f. Perekani mavuto awiri omwe Selina adakumana nawo chifukwa
chokomedwa.
________________________________________________________________
________________________________________________________________
(malikisi 2)
g. Nchifukwa chiyani Mangulenje adatenga nthawi yayitali
asanayankhe pamene Selina adamuuza kuti ndioyembekedzera?
________________________________________________________________
________________________________________________________________
(malikisi 2)
h. Kodi Mangulenje amatanthauzanji ponena mawu awa, ‘ndapeza
ndiwo’
________________________________________________________________
________________________________________________________________
(malikisi 2)

4
NAME __________________________________________ SCHOOL _______________________
i. Selina akadachita chani kuti apewe mavuto onse omwe adakumana
nawo?
________________________________________________________________
________________________________________________________________
(Malikisi 2)
j. Perekani ufulu uwiri omwe ophunzira amakhala nawo
________________________________________________________________
________________________________________________________________
(malikisi 2)

GAWO B (Malikisi 20)

2. Werengani nkhani ili m’munsiyi ndipo muyankhe mafunso otsatirawo:

Anthu onse pasiwa paja adali khumakhuma podziwa kuti tsikulo silitha
bwino. Atsibweni a Ndagona adaonetseratu kuti adali wokwiya kwambiri
ndi khalidwe la mpongozi wawo. Anthuwo adali maso yuu kunjira
kudikirira Mfumu Zathaizi yomwe inabwera kudzaonerera mwambo wosudzula
amake Ndaipalero, mkazi wa Ndagona.

Anthu ankangoyang’anizana. Amake Ndaipalero ndi ana awo asanu adali

khuma pafupi ndi khola la ngondolo. Kamodzikamodzi mayiyu ankamveka
kufwenthera kusonyeza chisoni chake komanso mantha. Katundu yense wa
m’nyumba ya Ndagona adali ataikidwa pamodzi. Amake Ndaipalero
sadaloledwe kugwira kanthu kalikonse ati kuopa kuti angasowetse
katundu wina m’nyumba muja. Mayiyu adatchuka ndi nkhanza kwa abale a
Ndagona. Anthu akuchimuna ankati mtengwa wawo sankakhala bwino ndi ana
ochokera kuchimunako. Chitsanzo chachikulu pakati pawo ankati adali
Chodziwadziwa, mwana wa Napichesi, mlongo wake wa malemu, amene
adalekera sukulu panjira atachokera kutawuni kumene ankakhala ndi
banja la Ndagona.

Chodziwadziwa atabwera kumudzi adauza anthu kuti adachoka kutawuni

kuja chifukwa amake Ndaipalero ankamuzunza kwambiri. Kumudzi kuja

5
NAME __________________________________________ SCHOOL _______________________
anthu adakhulupirira zonena za mwanayu ndipo adangoti adzaona pakuti
amake Ndaipalero adawachenjerera pogona.
Anthu akumudziwo sadadziwe kuti chifukwa chenicheni chimene
Chodziwadziwa adachokera kutawuni chidali chakuti iye ankathawa
apolisi.Chidachitika chidali chakuti, tsiku lina Chodziwadziwa ndi
anzake asanu adapita kukayenda ku masitolo a kutauni kuja. Ali
chiyendere, adakumana ndi ana a amwenye atatu amene adali kudya zakudya
zosiyanasiyana. Chodziwadziwa ndi anzake aja adalephera kuugwira mtima
ndipo adatsomphola zakudya zija n’kuvulaza mmodzi mwa ana a amwenyewo.
Kholo la mwanayo lidaimba lamya ku polisi ndipo posachedwa apolisi
adali nyomi pambuyo pa tiakapsala tija. Mwayi wa Chodziwadziwa udali
woti sadagwidwe, anzake onse aja adawakwidzinga unyolo.
Usiku watsiku limenelo Chodziwadziwa adalongeza katundu wake
natulukira pazenera, naubutsa wa kumudzi. Atafunsidwa kumudzi chomwe
adachokera kutawuni, iye adangotchula pavunda khola. Iye adanama kuti
wathawa nkhanza za amake Ndaipalero.

Mfumu Zathaizi idafika dzuwa likuswa mtengo. Iyo idabwera ndi nduna
ziwiri. Mfunseni, nduna Yachiwiri, adayamba kuyankhula, “Mosataya
nthawi tipemphe mkokowogona wakuchimuna kuti usudzule amake
Ndaipalero, zikomo”
“Ife, mfumu, tilibe mtunda wautali.” Mwatipeza adafotokoza. “Titakhala
pansi pamudzi pano tagwirizana kuti amake Ndaipalero ndi ana awo
abwerere kwawo pakuti mnzawo amene adawabweretsa kunoyo watsamira
mkono. Tiwasudzula ndi K50 iyi. Ndikatero ndaima. Mukafunsa za chuma
cha Ndagona, mayiyu ndi ana akewo satengapo kanthu. Iwowa zawo
adadyeratu wathu ali moyo.

Mfumu zathaizi idachita ngati yadzidzimuka kutulo ndipo idaimirira

mokwiya kwambiri, imvekere, “Mwatipeza, khala chete ndipo khala pansi!
Anthu adyera ndi oipa mtima ngati inu sindidawaone chibadwire changa!
Mukuwalanda chumachi, mukuganiza kuti azikathandizika ndi chiyani?
Kodi kumene Ndagona ndi mkazi wake ankapeza chumachi mudaliko?
Ndikudziwa kuti pamudzi pano muli ndi mangawa ndi mayiyu chifukwa cha

6
NAME __________________________________________ SCHOOL _______________________
zomwe adakuuzani Chodziwadziwa. Komatu leroleroli apolisi adali
kunyumba kwanga ndipo andiuza chifukwa chenicheni chimene nthyamba
wanuyu adachokera kutawuni. Si chifukwa cha amake Ndaipalero ayi, koma
chifukwa cha magwiragwira a mwana wanuyu! ndiye ine mfumu Zathaizi,
ndikuti chumachi ati atenge ndi mayiyu ndi ana ake. Inu yanu ikhala
nyumba yokhayi pakuti ili pamudzi panu. Igwani apa ndi…..”
Mfumu Zathaizi sidatsirize mawu ake, pakuti apolisi adangoti
balamunthu kutulukira. Chodziwadziwa adati ayesere kuthawa koma agalu
apolisi adamuwakha. Manyazi, mantha ndi chisoni zidawagwira anthu a
pamudzi paja. Adayamba kuchoka mmodzimmodzi, mitu ili werawera, manja
ali mkhosi.

Tsopano yankhani mafunso otsatirawa m’ziganizo zomveka bwino

a. Kodi nkhaniyi ikuchitikira kuti?

________________________________________________________________
(Malikisi 1)
b. Kodi nkhaniyi ili mu mphendero yanji?
_____________________________________________________malikisi 1)
c. Tsimikizani ndi mfundo ziwiri kuti atengambali ena munkhaniyi ndi
a nkhanza.
________________________________________________________________
________________________________________________________________
(Malikisi 2)
d. Tsimikizani, popereka mfundo ziwiri zosonyeza kuti Chodziwadziwa
adali ndi khalidwe loipa.
________________________________________________________________
________________________________________________________________
(Malikisi 2)
e. Perekani zipangizo za nkhani zamchezo ndi zolembedwa ziwiri zomwe
mlembi wagwiritsa ntchito
________________________________________________________________
________________________________________________________________
(Malikisi 2)

7
NAME __________________________________________ SCHOOL _______________________
f. Tchulani chifukwa chimodzi zomwe Mfumu Zathaizi adapereka kuti
ateteze katundu wa amake Ndaipalero ndi ana awo.
________________________________________________________________
(Malikisi 1)
g. Tsimikizani mfundo yakuti ‘zakumva zipweteketsa mutu’ malinga ndi
nkhaniyi.
________________________________________________________________
_______________________________________________________________
(Malikisi 1)
3. Werengani ndakatulo ili m’munsiyi ndipo muyankhe mafunso
otsatirawo.

Nzeru za antu n`zozungulitsa

Tsengalo! Tsengalo! Onani

Achita zododometsa ena
Ngiri! Ngiri! pompo Nginde
Pa mikombero iwiri ayenda
Nee! monga asambira
La la la! mlalu ona
Nzeru za anthu n`zozungulitsa

Mwaona mikombero ya moto

Ikalipa poti iyende
Kuopsa itulutsa utsi
Sontho! ulendo kukalipa siileka
Wozungulitsa ali pamsana
Thu! Thu! Thu! wautali
Nzeru za anthu n’zozungulitsa

Anzanganu onani chinanso

Nyumba yamikombero

8
NAME __________________________________________ SCHOOL _______________________
Iyenda nibangula vuu!
Chamva ludzu achipatsa madzi
Kodi ichochi n`chamoyo?
Hii muli anthu mkatimo
Mzeru ya anthu njododometsa

Nanga n’chiyaninso timangachi?

Njanje, atero kapitawo
Kunzimbe akuti ziliko
Nyumba zoyenda panjanje
Lero kuno ifika kaya?
Zokaikitsa
Luso la anthu ndi lodabwitsa.

Tsopano yankhani Mafunso otsatirawo

a. Tchulani mtundu wa ndakatuloyi malingana ndi kayalidwe

_______________________________________________(malikisi 1)

b. Fotokozani zinthu ziwiri zomwe zamudabwitsa mlembiyu

m’chichewa chomveka bwino.
___________________________________________________________
___________________________________________________________
(makikisi 2)

c. Kodi mawu akuti Mikombero akutanthauzanji mu ndakatuloyi

______________________________________________(malikisi 1)
d. Perekani chitsanzo chimodzi cha zipangizo za ndakatulo
zotsatirazi kuchokera m’ndakatuloyi
i) Funso la chodziwadziwa
___________________________________________________
ii) Mvekero
________________________________________(malikisi 2)

9
NAME __________________________________________ SCHOOL _______________________
e. Perekani zipangizo zina ziwiri za nkhani zamchezo ndi
zolembedwa zomwe mlembi wafewetsera luso lake kupatula
zatchulidwa mu funso d.
___________________________________________________________
___________________________________________________________
(malikisi 2)
f. Tsindikani mwambi wakuti, ‘kusadziwa n’kufa komwe’
molingana ndi ndakatuloyi.
___________________________________________________________
___________________________________________________________
(malikisi 2)

GAWO C (Malikisi 10)

4. Werengani nkhani yotsatirayi mosamala ndipo mufupikitse kuti

ikhale ndi mawu osachepera 14 koma asapitilire 20.

ANTHU OCHITA MALONDA

Anthu amachita malonda osiyanasiyana padziko pano. Pali malonda
monga ogulitsira m’sitolo,kugulitsa zovala, kugulitsa zakudya ndi
zina zambiri. Malondawa amagulitsidwa malo osiyamasiyana. Ena
amayendayenda ndi katundu wawo kulondola ogula, ndiponso ena
amangokhala m’mbali mwa njira kapena msewu. Onsewa amayembekeza
kutolera pakutha pa tsiku lililonse. Ochita malonda amakumana ndi
mavuto osiyanasiyana monga kuberedwa ndalama ndi akuba komanso
achitaka, kulipira misonkho yokwera komanso kuonongeka kwa katundu
akakhalitsa. Vuto limodzi lomwe limawadetsa nkhawa yosaneneka ndi
m’mene adzayendere kukafika kumsika wina makamaka kukakhala
kutali. Nkhawa bii chifukwa cha mmene adzanyamulire katundu monga
mabelo a zovala, matumba a mtedza, chimanga, mbatata, mawere,
maungu ndi zipangizo zomangira nyumba monga zitseko ndi mazenera,
zomwe zimangoti mbwee pa msika.

________________________________________________________________

10
NAME __________________________________________ SCHOOL _______________________
________________________________________________________________
________________________________________________________________
________________________________________________________________
________________________________________________________________
________________________________________________________________
________________________________________________________________
________________________________________________________________
________________________________________________________________
________________________________________________________________
(malikisi 5)

5. Masulirani nkhani ili m’munsiyi m’chichewa chomveka bwino.

Modern services are produced because of science and technology.

These include solar power, use of computers and cellular phones.
Malawians are able to communicate using cellular phones. People
have installed solar power in villages. They are now able to
operate small scale businesses like video shows

(malikisi5)

MAFUNSO ATHERA PANO

11

You might also like