Professional Documents
Culture Documents
Chichewa Paper II
Chichewa Paper II
CHICHEWA
PEPALA LACHIWIRI
Monday, 30 May, 2022 (Malikisi 50) Subject Number: J 032/II
1. Onetsetsani kuti
Nambala Chongani Osalemba umu
pepalali lili ndi
ya funso mafunso
masamba asanu ndi
okhawo
anayi ndipo lili
omwe
mmagawo atatu, A, B,
mwayankha
ndi C.
1
2. Yankhani mafunso
onse mu gawo A, B 2
ndi C.
3
3. Lembani dzina lanu
pamwamba pa tsamba 4
lililonse. 5
4. Perekani pepala lanu Total
kwa woyang’anira
mayeso nthawi yolembera mayeso ikatha.
Page 1 of 9
Gawo A (Malikisi 20)
KUMVETSA NKHANI
M’dziko mumo komanso mayiko ena a mu Africa anthu amakhala ndi zikhulupiliro
zosiyanasiyana. Nthawi zina anthu ochita kafukufuku amangoti anthu a ku Africa ndi anthu
odalira miyambo ndi zikhulupiliro. Izi zingathe kukhala zoona koma sizitanthauza kuti
anthu amitundu ina alibe miyambo ndi zikhulupiliro zawo ayi.
Miyambo ngati yoletsa amayi kukachilira kuchipatala nthawi yawo yikakwana ndiyo
yatsitsira ntchembere zambiri kulichete. Ndi chifukwa chake Boma ndi mabungwe
osiyanasiyana komanso mipingo zili pakalikiliki kudziwitsa anthu za kuopsa kwa miyambo
ina ngati imeneyi.
Chinthu chofunika kudziwa ndichakuti zinthu zimasintha. Ngakhale miyambo yakhala ili
chomwecho, zinthu zambiri zasinthasintha. Anthu achulukana koposa momwe adalili kale
ndipo zitukuko zosiyanasiyana zachitika. Mitengo yambiri yomwe anthu ankadalira ngati
mankwala idasowa. Choncho kukakamira ina mwa miyamboyi ndi zikhulupiliro zakalezo
ndikulimbira mtunda opanda madzi.
Page 2 of 9
Tsopano yankhani mafunso otsatirawa.
(a) N’chifukwa chiyani anthu aku Africa sayenera kudziwika monga anthu odalira
miyambo ndi zikhulupiliro?
______________________________________________________________________
_______________________________________________________________________
(malikisi 2)
(b) Kodi kufunika kwa miyambo ndi zikhulupiliro ndi kotani? Perekani kufunika kuwiri.
i.
_____________________________________________________________________
_____________________________________________________________________
(malikisi 2)
ii.
_____________________________________________________________________
_____________________________________________________________________
(malikisi 2)
ya anthu.
i.
_____________________________________________________________________
______________________________________________________________________
(malikisi 2)
ii.
_____________________________________________________________________
_____________________________________________________________________
(Malikisi 2)
Page 3 of 9
(d) Mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani padali zikhulupiliro zoletsa ana kudya mazira?
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
(malikisi 1)
(e) Kodi Boma ndi mabungwe athandiza bwanji kulimbana ndi zikhulupiliro zokhudza
kuchira kwa amayi?
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
(malikisi 2)
i. mafirika __________________________________________________________
(malikisi 2)
______________________________________________________________________
(malikisi 2)
______________________________________________________________________
_____________________________________________________________________
(malikisi 2)
____________________________________________________________________
(malikisi 1)
Page 4 of 9
Gawo B (Malikisi 20)
Chibingwe adangoti pakamwa gwii ndipo kenako misozi idalengeza m’maso. Iye
sadayembekezere kuti mlamu wake angamutsukuluze chotero. Mkazi wake Naphiri
ankangokondwera ndi mfundo iliyonse yomwe mchimwene wake adali kuyankhula.
Kawiri kapena katatu konse adayankhira movomereza mchimwene wake. “Ndizoona,
ndiwo mawu a mwamuna awa achimwene.” “ Uyu ndi mlongo wanga, mzime wa m’banja
mwathu. Iyeyu adaponda pamutu pangapa. Ukamandiona ine uzidziwa kuti waona Soga,
mwini mbumba. Usandione kutuwaku, ndimadya zanga ine. Kwanuko kudalibe mbeta zoti
ukadakwatira n’kumazilamulira? Ukachita masewera ndikuyatsira mwatso masana;
usandilowe ngati thekenya.
“Ndamva kuti umamunamiza mlongo wanga kudya galu. Umati akangotula mtolo ali
nawowu basi akatseketse. Akuti umati ana asanu basi akwana. Kodi ana a munthu amachita
kuwerenga ngati mandanda a nkhuku? Akutinso umati popeza iyeyu wakukanira
kukatseketsa umati ndiwe ukatseketse. Kodi ndiwe imbwa kapena ng’ombe yapajoko kuti
ukatseketse? Ndadziwa, ufuna kuti mlongo wanga anthu azimuyoyorera mnyozo kuti
adakwatiwa ndi mtheno. Ndi umunthu ukuchita iwewu?”
Chibingwe adakwatira pamudzi wa a Kombo zaka zisanu zapitazo ndipo banja lake lidali
kale ndi ana anayi. Chaka chilichonse ankabereka. Izi zinkamusangalatsa kwambiri mlamu
wake, Soga, yemwe ankati mbumba yake izikula.
“Achikhala kuti ufumu amalowera kukula kwa mbumba, chaka chino nkadaunyantha.
Ufumu tizilowa ndife oswana ngati mbewa. Ena angoyenda tumbwatumbwa m’muno
chikhalirecho alibe ndi mdzukulu yemwe.” Ankalalata chotere Soga akadakwa.
Soga adali ng’oma ya m’mudzi mwa a Kombo kaamba koti adali mbiyang’ambe. Umphawi
ndi njala zidali abwenzi a banja lake chifukwa adalibe nthawi yogwira ntchito. Kukacha
Page 5 of 9
amangoganiza za mowa. Mkazi wake adamuthawira asadachembeze n’komwe kaamba ka
uchidakwa ndi unyopo. Nthawi zambiri Soga ankadya nsima kwa mlamu wake.
Atadya mutu, Chibingwe adayankhula, “Ndamva mawu anu onse. Zonse akuuzani alongo
anu ndi zoona. Ine ndimavutika kwambiri kupeza zofunika pa banja pano. Mayiwa akamwa
madzi ndiye kuti mnyumba muno tikhalamo anthu asanu ndi awiri. Pa nkhani yachakudya
ndiye kuti tikhalamo asanu ndi atatu. Zikundivuta kwambiri…”
“Thula! Khala chete, mlesi!” Soga adamudula m’kamwa mlamu wake. “Iwe ulibe
ulamuliro pabanja pano. Pamudzi pano usamayese kuti mpazitsiru kuti uzikulirapo
mwendo. Umavutika chiyani pano? Amavutika ndi mlongo wanga. Kodi umamuthandiza
kusenza ndi kutula mitolo?”
Chibingwe ataona kuti mlamu wake wamkitsa nacho chipongwe adamanga katundu wake.
Iye sadatsanzike munthu wina aliyense ndipo sakudziwika komwe adalowera.
________________________________________________________________________
(malikisi 1)
______________________________________________________________________
______________________________________________________________________
(malikisi 2)
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
(malikisi 2)
________________________________________________________________________
(malikisi 1)
________________________________________________________________________
(malikisi 1)
________________________________________________________________________
(malikisi 1)
Otsatirawo.
KUSIMBA TSOKA
One day, Hyena visited Antelope. Hyena told him that he wanted them to become friends.
But in reality, Hyena never wanted them to be friends. He wanted to eat Antelope because
Antelope was big and plumb.
Page 8 of 9
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
(malikisi 5)
5. Fupikitsani kankhani kali m’munsika kuti kakhale ndi mawu osachepera 11 koma
asapitilire 15.
Nyamata wamtali kwambiri uja, uja nthawi zonse amayenera kuwerama kuti adutse
pakhomo la nyumba yakwathu ija, akuti abwera masiku awiri akubwera kutsogoloku ndi
Joni, Masiye ndi Mavuto kuti azatenge tanaposi, mpiru, mkhwani ndi kabichi.

Page 9 of 9