Download as pdf or txt
Download as pdf or txt
You are on page 1of 8

Republic of Zambia

MINISTRY OF EDUCATION

MAYESO AKUDZIWA KUWERENGA


NDI KULEMBA A GIREDI 1 MU
2024

CINYANJA
KABUKU KA MPHUNZITSI
KAMALANGIZO NDI MAFUNSO

TEMU 2

SABATA LA 5
MALANGIZOAMPHUNZITSI:

1. Tsiku lamayeso lisanafike, muyenera kuwerengamo m’kabuku ka


mphunzitsi kamalangizo ndi mafunso kuti mudziwe bwino-bwino
zam’katimo. Dziwani kuti funso la nambala 9 ndi 10 lifuna kuti
muonetse zinthu kwa aphunzi; konzekerani zinthuzo mayeso
asanayambe.
2. Werenga funso liri lonse kawiri mwaluso ndiponso mosamala
momwe lalembedwera m’buku lamayeso.
3. Onetsetsa kuti aphunzi amvetsetsa funso bwino-bwino ndipo
ayankha musanapite pafunso lina.
4. Uyenera kupereka mayeso kwa aphunzi onse m’kalasi mzigawo A
ndi B. Zigawo C, D, E ndi F perekani mayeso kwa aphunzi m’modzi-
m’modzi.

5. Nthawi yamayeso siinaikidwe, koma mayeso a mkalasi a zigawo


A ndi B angatenge theka la ola limodzi. Mayeso am’modzi-
m’modzi azigawo C, D, E ndi F angatenge mphindi ziwiri kapena
zitatu(2–3 minutes) pa mphunzi ali yense.
6. Usanayambe kupereka mayeso, lemba zigawo A ndi B momwe
ziriri mkabuku kamphunzi pa bolodi kotero kuti aphunzi athe
kulondola.

MALANGIZO K W A APHUNZI:
Tidzacita nchito. Nchitoyi ndi yamamvekero, kuwerenga ndi
kulemba.
Ndidzakufunsani mafunso okhudza zomwe ndi dzanena kwainu
ndi zomwe mudza werenga.
Tidzacita izi mwakanthawi kocepa. Mudzalemba mayankho
m’mabuku anu. Kodi ndinu wokonzeka kuyamba?

2
Mphunzitsi: Onetsetsa kuti aphunzi onse ndi okonzeka kulemba mayeso
poona kuti:
 Ali ndi mabuku olembamo ndi ma pensulo
 Atha kuona bwino zolembedwapa bolodi.

3
CIGAWO A: MVEKERO (PHONICS)
1. Uza aphunzi: Onani pa nambala1 iri pa bolodi. Pali mamvekero.
Ndidzachula mvekero. Sankhani mvekero imene ndidzachula pama
mvekero apatsidwa muti mabokisi. Lembani yankho m’mabuku anu.
Mvekero ndi j
v s j

Yankho: j
2. Uza aphunzi: Onani pa nambala 2 iri pa bolodi. Pali mamvekero.
Ndidzachula mvekero. Sankhani mvekero imene ndidzachula mvekero
zapatsidwa mutimabokisi. Lembani yankho m’mabuku anu. Mvekero ndi
mb

kh mb mw

Yankho: mb
3. Uza aphunzi: Onani pa nambala 3 iri pa bolodi. Pali masilabe.
Ndidzachula silabe. Sankhani silabe imene ndizachula pamasilabe
apatsidwa pa bolodi. Lembani yankho m’mabuku anu. Silabe ndi la

na la ga

Yankho: la

4. Uza aphunzi: Onani pa nambala 4 iri pa bolodi. Pali mau. Ndidzachula


silabe. Sankhani liu pa mau apatsidwa pa bolodi limene liri ndi silabelo.
Lembani liulo m’mabuku anu. Silabe ndi bo

moto kama bola

Yankho: bola

4
5. Uzani aphunzi: Onani pa nambala 5 iri pa bolodi. Pali liu. Lembani
nambala yamasilabe ali mliu m’mabuku anu. Liu ndi: cake

3 2 1

Yankho: 2

CIGAWO B: KULEMBA (WRITING)


6. Uza aphunzi: Onani pa nambala 6 iri pa bolodi. Pali lemba. Lembani
lemba m’mabuku anu. lemba ndi: k

Yankho: k

7. Uza aphunzi: Onani pa nambala 7 iri pa bolodi. Pali silabe. Lembani


silabe m’mabuku anu. silabe ndi: kha.

Yankho: kha

8. Uza aphunzi: Onani pa nambala 8 iri pa bolodi. Pali liu. Lembani liu
m’mabuku anu. Liu ndi: mwezi

Yankho: mwezi

CIGAWO C: MAU (VOCABULARY)


9. Uza mphunzi, Ndidzakuonetsani cinthu. Ndifuna kuti undiuze dzina la
cinthu ndidzakuonetsa. Cinthu ndi ici…. (onetsa buku).

Yankho: buku
10. Uza mphunzi: Ndidzakuonetsani ciwalo cathupi cimodzi. Ndifuna kuti
undiuze dzina la ciwaloco. Ciwalo ndi ici…. (onetsa cala)

5
Yankho: cala

11. Uza mphunzi. Nyumba ndi zambiri, imodzi timati ……

Yankho: Nyumba

CIGAWO D: KUZINDIKIRA MVEKERO (PHONEMIC AWARENESS)

12. Uza mphunzi: Ndidzachula silabe. Ndifuna kuti undiuze mvekero yomwe
uzamva koyambilira kwa silabe. Silabe ndi: nde

Yankho: nd

13. Uza mphunzi: Ndidzachula liu. Ndifuna kuti undiuze mvekero yomwe
uzamva koyambilira kwa liu. Liu ndi: phata

Yankho: ph

14. Uza aphunzi: Ndidzachula mau atatu. Ndifuna kuti undiuze liu limene
liri ndi mvekero losiyana ndi mau ena koyambilira. Mau ndi awa: phale,
mbuzi, phula

Yankho:. mbuzi

6
CIGAWO E : MVETSERO (LISTENING COMPREHENSION)

Uza mphunzi: Ndidzawerenga kankhani kawiri kwaiwe. Ndikatha


ndidzakufunsa mafunso anai. Uyankhe mafunso omwe ndidzafunsa.
Sankha yankho loyenera pa mau apatsidwa m’mabokosi. Tsopano
mvetsera kankhani aka.

Nkhani
Jemusi wapita mocedwa ku sukulu lero.
Aphunzitsi anamfunsa cifukwa ninji anacedwa.
Jemusi anati, anacedwa cifukwa sanali kumva bwino.
Aphunzitsi anapereka Jemusi kuchipatala

Tsopano ndidzakufunsani mafunso.

15. Kodi ndani anapita mocedwa kusukulu?


Yankho: Jemusi

16. Ndani anafunsa cifukwa ciani anapita mocedwa ku sukulu?

Yankho: Aphunzitsi

17. Cifukwa ninji Jemusi anapita mocedwa ku sukulu?

Yankho: anadwala

18. Kodi aphunzitsi anampereka kuti Jemusi?

Yankho: ku chipatala

7
CIGAWO F: KUWERENGA MOSAMALA (FLUENCY)

19. Uza mphunzi: Ndidzakuonetsa silabe. Werenga silabe mokweza ndi


mofulumira. Ndidzakupatsa kanthawi kocepa (masekondi 5)
kuwerenga silabe. (Onetsa khadi liri ndi silabe kwa mphunzi) silabe
ndiiri: khe

20. Uza mphunzi: Ndidzakuonetsa liu liri. Werenga liu mokweza ndi
mofulumira. Ndidzakupatsa kanthawi kocepa (masekodi 5) kuwerenga
liu. (Onetsa khadi liri ndi liu kwa mphunzi) Liu ndi iri; dzira.

MAYESO ATHA

You might also like