Download as pdf or txt
Download as pdf or txt
You are on page 1of 9

DZINA_____________________________________________________________KALASI_____

2020 MALAWI SCHOOL CERTIFICATE OF EDUCATION

CHICHEWA
PAPER II
(Malikisi 90 )
Subject Number: MO32/II
Time Allowed 2 Hours

Malangizo:
1. M’gawo A: Malamulo a Chiyankhulo : Yankhani mafunso onse
(Malikisi 40)
2. M’gawo B : Kumvetsa nkhani :Yankhani mafunso onse.
(Malikisi20)
3. M’gawo C : Chifupikitso. (Malikisi 15)
4. M’gawo D : Chimasuliro ( Malikisi 15)

1
DZINA_____________________________________________________________KALASI_____
GAWO A (Malikisi 40)

MALAMULO A CHIYANKHULO.
Langizo: Yankhani mafunso onse.

1. Lembani ziganizo zokhala ndi “ li “ amene akugwira ntchito zotsatirazi ndipo mutseke
mzere kunsi kwake
a. Kukhala tsinde la mneni
_______________________________________________________________

(Malikisi 2)
b. Kukhala mgwirizanitsi wamchitantchito
_______________________________________________________________
_______________________________________________________________
(Malikisi 2)
c. Kukhala mgwirizanitsi wamtchitidwantchito
_______________________________________________________________
_______________________________________________________________
(Malikisi 2)
d. Kukhala mgwirizantsi wamawerengo
_______________________________________________________________
_______________________________________________________________
(Malikisi 2)
e. Kukhala mphatikiramtsogolo woloza
_______________________________________________________________
_______________________________________________________________
(Malikisi 2)

2. Perekani mitundu ya akapandamneni amene ali ndi mizere kunsi kwawo mziganizo
zotsatirazi
i. Ine ndi bambo anga tipita kumunda.
_____________________________________________________________
(Malikisi 2)
ii. Mpeni wanga watsopano uja wasowa .
_______________________________________________________________
(Malikisi 2)
iii. Iwo amayankhula mopsetsa mtima .
_____________________________________________________________
(Malikisi 2)
iv. Mayi uja adakwatiwa ndi mzungu .
_______________________________________________________________

(Malikisi 2)
v. Kusamalira zachilengedwe ndi chinthu chabwino .
_____________________________________________________ (Malikisi 2)
3. Sinthani ziganizo zotsatirazi kuchoka ku zoyankhula wina kupita ku zoyankhula
mwini

2
DZINA_____________________________________________________________KALASI_____
i. Chiphiko wati iye ndi mwana wake anabwera dzulo lakelo.
_______________________________________________________________
_______________________________________________________________
_______________________________________________________________
(Malikisi 2)
ii. Amayi ati iwo amafuna kugula chimanga chija tsikulo.
_______________________________________________________________
_______________________________________________________________
_______________________________________________________________
(Malikisi 2)

iii Mlendoyo adati dziko lathu ndi la mtendere.

_________________________________________________________________

__________________________________________________________________

iv Iye adafuna kudziwa chomwe iwo adali kuphika

_________________________________________________________________

__________________________________________________________________

( Malikisi 2 )

v. Maliya adadabwa ngati iye akadatha kufika kuja tsiku lotsatiralo.

__________________________________________________________________
________________________________________________________( Malikisi 2)

4. Phwanyani chiganizo chotsatirachi powunika mawu pawokhapawokha.

Iye wagula chipewa .

___________________________________________________________________________

. (Malikisi 10)

3
DZINA_____________________________________________________________KALASI_____

GAWO B (Malikisi 20)

Kumvetsa Nkhani ndi Kusanthula Chiyankhulo.

5. Werengani nkhani ili m’munsiyi mosamala ndipo muyankhe mafunso
otsatirawo.

Kunja kudacha bwino ,kamphepo kayaziyazi kadali kuomba kuchokera mphiri la chitunda
.M‟mudzi mwa Zagwazatha aliyense sadadziwe kuti tsikulo libala chiyani choncho
amkangoti kudziko kulinji ?

Mwadzidzidzi kudamveka kukuwa motere : Msonkhano ! Msonkhano kubwalo la mfumu

masana ! Nonse mubwere mwaunyinji .Amene sabwera aona chomwe chidameta nkhanga
mpala” Aliyense uthenga wa msonkhano udampeza ndipo ankangodikirira nthawi kuti
akamve chomwe mfumu yawo imafuna kukawayankhula .

Nthawi ikuyandikira anthu adali dululudululu kulunjika kwa mfumu .Ana amayi ,abambo
komanso agogo adali odwabwa ndi msonkhano wadzidzidziwu .Mmene nthawi ya
msonkhano imakwana ,pabwalo pa mfumu padali posowa mphondero ndipo onse adangoti
maso gaa pa mfumu yawo kuti iyankhula zotani .Anthu onse adatchera makutu awo kuti
amve uthenga womwe mfumu yawo idali nawo .

Posakhalitsa mfumu ndi nduna zake zitatu : Kalionera ,Mchambe ndi Tongole adatulukira
.Nkhope ya mfumuyi idali yakugwa mwina chifukwa cha mphamvu ya uthenga umene
imafuna kuti itulire anthu ake .Anthu onse adaimilira ataona mfumu yawo ndi nduna zake
zikubwera .Itakhala pansi onse adakhalanso .

“Moni nonse “ ,adayamba motero a Tongole ndipo adapitiliza ndi kuti “ anthu nonse muli
olandilidwa pa bwalo lino .Mfumu yathu yatiitana tonse kuti tikambirane nkhani imene
yakhudza tonse dera lino . Mfumu yathu isanaimilire ndifuna ndikupempheni nonse kuti gogo
wathu akaimilira ndi kuyamba kuyankhula ,pasapezeke osokoneza kuti tingatenge za
m‟maluwa .Amene satsatira izi alandira chilango chowawa .Tsono posachulutsa gaga m‟diwa
ndipemphe mfumu yathu kuti itiyankhule “.Atatero Tongole adakhala pansi .

Mfumu zagwazatha idayamba yakonza chisoti chake komanso mkanjo wake .Itaimilira
,idatsuka kukhosi potsokomola n‟kuyamba kuyankhula .”Amayi ndi abambo ,lero ndili ndi
chisoni komanso manyazi ndi nkhani yomwe yachitika m‟mudzi muno. Mukudziwa nonse
kuti tili ndi chitukuko chomanga midadada ya sukulu pa sukulu ya Kadzimete .Tonse tidali
chimwemwe tsaya pamene Bwanankhubwa adalengeza kuti boma lidatipatsa ndalama
miyandamiyanda zomangira midadada ya sukulu ya Kadzimete .Pofuna kuti ntchito iyende
mwadongosolo ,tidasankha bungwe loyendetsa chitukukochi .Wapampando wa bungweli ndi
a Mwataya .Poyamba zinthu zidali bwino ndipo aliyense amangoti zimatere bwenzi zinthu
zikoma .Zoonadi mtima wa mnzako ndi tsidya lina .Ife tonse tidali mtulo .Bungwe lomwe
limayendetsa ntchitoyi limangoti “ taupeza mgodi wosatha chuma .”

Mfumu Zagwazatha idakhala phee kenaka idaitanitsa madzi akumwa kwa Kalionera ,nduna
yake .Itamwa madzi ,idapitiliza kuyankhula .”Anthu nonse mudziwe ichi kuti mbiri
sigonera.Bungwe lomwe ife tidalikhulupilira lamveka ndi fungo loipa .Inde umanena
chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga .Lero mbandakucha kunabwera wapolisi wa
boma kudzandiuza kuti munthu wina wawanong‟oneza kuti m‟manda mwathu muli dzenje
4
DZINA_____________________________________________________________KALASI_____
lalikulu limene mudabisidwa matumba a simenti amene adabedwa ku chitukuko cha
midadada yasukuku .Nditamva izi thupi langa linagwidwa dzanzi .Sindinalekere pompo
.Ndinatengana ndi wapolisiyo ndi nduna zanga zonse kukawona malodzawo .Titangofika
kumandako ,takapeza chidzenje chili pululu ,matumba a simenti ali ngundangunda .Tonse
misozi inatsanuka ngati madzi a mu mtsinje wa Shire .

Pochoka kumandako , tinadzera kwa wapampando wa chitukuko cha midadada ya sukulu

.Titafika pa nyumba ya a Mwataya ,takapeza iwowa akulowetsa matumba a simenti
mnyumba mwawo ndipo analephera kuyankha za komwe adawatenga matumbawo
.Ndikukamba pano Mwataya ali mmanja mwa apolisi ndipo atsekeredwa podikira kukalowa
mkhoti.

Mfumu ikuyankhulabe ,munthu wina dzina lake Zaululuka adangoimilira nanena kuti “pepani
mfumu ,khoswe wapadenga adaululitsa wapadzala .Anthu amenewa ndi kale adayamba kuba
.Inenso ndidawapezako akugulitsa simenti kwa bambo Mwaononga womwe akhala apowo .

Bambo Mwaononga adafunsidwa ndi mfumu Zagwazatha ngati nkhaniyo idali yoona .A
Mwaononga adangokhala duu kusowa choyankha .Apa mfumu idalamula kuti a Mwaononga
amangidwe chifukwa cha utambwali wawo .

Pomaliza mfumu idalamula gulu lonse kuti lipite kumanda komanso kunyumba kwa
Mwaononga kukawona katundu wobedwayo .Zidali zomvetsa chisoni aliyense manja ali
mkhosi ,maso ali pa matumba asimenti kwinaku akumvera Mwaononga akuchita mbewewe
poyankha mafunso omwe amafunsidwa ndi apolisi .Matumba asimentiwo adanyamulidwa pa
ngolo ya amfumu ndipo bungwe latsopano loyang‟anira chitukuko lidasankhidwa .Mtsogoleri
wake adali Zaululuka .

Tsopano yankhani mafunso otsatirawa m‟ziganizo zomveka bwino .

a. (i) Kodi nkhaniyi idachitikira mudzi uti ?

________________________________________________________________________

( Malikisi 1)

(ii) Ndi mawu ati m‟nkhaniyi omwe akusonyeza kuti mneneri wa mfumu

adapereka uthenga moyenera ?

_______________________________________________________________________
______________________________________________________________(Malikisi 2 )
(iii) Perekani chifukwa chimodzi chomwe chidachititsa kuti anthu apite ku msonkhano
mwaunyinji ?

________________________________________________________________________
________________________________________________________________________

5
DZINA_____________________________________________________________KALASI_____
________________________________________________________________________

( Malikisi 2 )

(iv) Lembani nduna zitatu zokha za mfumu Zagwazatha .

________________________________________________________________________

( Malikisi 3 )

(v) N‟chifukwa chiyani nkhope ya mfumu Zagwazatha idali yakugwa ?

________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________

( Malikisi 2)

(vi) Lembani njira imodzi yomwe anthu amaperekera ulemu kwa mfumu yawo
mnkhaniyi?

______________________________________________________________________

_______________________________________________________________________

( Malikisi 2 )

( vii) N‟chifukwa chiyani a mfumu ndi nduna zawo adalira kumanda kuja ?

________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________

( Malikisi 2)

(viii) Kodi mawu akuti „ Ife tonse tidali m‟tulo‟ akutanthauza chiyani malingana ndi
nkhani
________________________________________________________________________
______________________________________________________________(malikisi 2)

(i) Pezani mawu amodzi mnkhaniyi womwe akufanana ndi mawu awa :

1. “chibwibwi “______________________________________________
2. “duu” ________________________________________________
( Malikisi 2)

(ii) Perekani nsinjiro mnkhaniyi zomwe matanthauzo awo ndi awa :

6
DZINA_____________________________________________________________KALASI_____
(i) “ akhaula” ________________________________ ( Malikisi 1)
(ii) “mbiri yoipa “ ____________________________ ( Malikisi 1 )

GAWO C (Malikisi 15)

6. Werengani nkhani yotsatirayi mosamala. Ili ndi mawu 146 ndipo muyifupikitse kuti
ikhale ndi mawu osachepera 68 koma asapitirire 78

KODI MALAWI AKUPAMBANA PA NTCHITO YOLIMBANA NDI ZIPHUPHU .

Dziko la Malawi lili pa nkhondo yaikulu yolimbana ndi amaliwongo ambiri omwe akuvutitsa
anthu ake komanso akubwezeretsa chitukuko cha dzikoli m‟mbuyo .Amaliwongowo ndi
zinthu monga izi : matenda a edzi ndi malungo ,imfa zauchembere,kuonongeka kwa zinthu
zachilengedwe ,kusintha kwa nyengo ,katangale ndi ziphuphu,umphawi komanso kulekera
sukulu panjira kwa ophunzira ambiri mu sukulu za pulayimale .

Chaka chino cha 2020 kwamveka nkhani yosangalatsa. Zotsatira za kafukufuku yemwe
adachitika miyezi isanu yapitayo pa nkhani yaziphuphu ,zikuonetsa kuti dziko la Malawi
likukhala ngati likupambana pa nkhondo yolimbana ndi mchitidwe waziphuphu poyerekeza
ndi momwe zinthu zidalili zaka zam‟mbuyomu.

Bungwe la anthu ena a ntchito zamalonda lolimbana ndi ziphuphu mdziko muno ,lotchedwa
Pamtetete ,lidapempha bungwe lazakafukufuku la Tifufuze kuti liunike momwe zinthu zilili
pa nkhani ya ziphuphu mdziko muno .Bungwe la Tifufuze lidafufuza nthambi zaboma
zokwana makumi atatu ndipo lidapeza kuti nthambi zisanu zokha ndi zomwe zikupitirizabe
kuchita ziphuphu kwambiri.

7

GAWO D : CHIMASULIRO ( Malikisi 15 )

7. Masulirani nkhani ili m‟munsiyi m’chichewa chomveka bwino.

HOW SMOKING AFFECTS YOUR BODY.

Smoking is the biggest cause of preventable deaths in Malawi. Smoking damages your heart
and your blood circulation. Carbon monoxide from the smoke put strain on the heart by
making it work faster. Smoking cigarettes can damage a female‟s reproductive system and
make it more difficult to get pregnant . Your lungs can be very badly affected by smoking.
Smoking can cause problems such as bad breath and stained teeth.

The good news is that after only one year of not smoking, your risk is reduced by half.

8

MAFUNSO ATHERA PA TSAMBA LINO

You might also like